Yobu alinganiza chikhalidwe chake chakale ndi tsoka latsopano, nalimbika kuti sanachite zotchulidwazi
1 Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wake, nati,
2 Ha! Ndikadakhala monga m’miyezi yapitayi,
monga m’masiku akundisunga Mulungu;
3 muja nyali yake inawala pamutu panga,
ndipo ndi kuunika kwake ndinayenda mumdima;
4 monga umo ndinakhala m’masiku anga olimba,
muja uphungu wa Mulungu unakhala pahema panga.
5 Muja Wamphamvuyonse akali nane pamodzi,
ndi ana anga anandizinga;
6 muja popondera ine padakhatamira ndi mafuta amkaka,
ndi thanthwe linanditsanulira mitsinje ya mafuta a azitona!
7 Muja ndinatuluka kunka kuchipata kumzinda,
muja ndinakonza pokhala panga kukhwalala,
8 anyamata anandiona nabisala,
okalamba anandinyamukira, nakhala chilili.
9 Akalonga anadziletsa kulankhula,
ndi kugwira pakamwa pao;
10 mau a omveka anali zii,
ndi lilime lao linamamatira kumalakalaka ao.
11 Pakuti pondimva ine khutu, linandidalitsa;
ndipo pondiona diso, linandichitira umboni.
12 Pakuti ndinapulumutsa wozunzika wakufuula;
mwana wamasiye yemwe wosowa mthandizi.
13 Dalitso la iye akati atayike linandidzera,
ndi mtima wa mkazi wamasiye ndinauimbitsa mokondwera.
14 Ndinavala chilungamo, ndipo chinandivala ine;
chiweruzo changa chinanga mwinjiro ndi nduwira.
15 Ndinali maso a akhungu,
ndi mapazi a otsimphina.
16 Ndinali atate wa waumphawi;
ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwe ndinafunsitsa.
17 Ndipo ndinathyola nsagwada ya wosalungama,
ndi kukwatula chogwidwa kumano kwake.
18 Pamenepo ndinati, Ndidzatsirizika m’chisa changa;
ndipo ndidzachulukitsa masiku anga ngati mchenga.
19 Muzu wanga watambalala kufikira kumadzi;
ndi mame adzakhala pa nthambi yanga usiku wonse.
20 Ulemu wanga udzakhala wosaguga mwa ine,
ndi uta wanga udzakhala wosalifuka m’dzanja mwanga.
21 Anthu anandimvera, nalindira,
nakhala chete, kuti ndiwapangire.
22 Nditanena mau anga sanalankhulenso,
ndi kunena kwanga kunawakhera.
23 Anandilindira ngati kulindira mvula,
nayasama pakamwa pao ngati kulira mvula ya masika.
24 Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima;
ndipo sanagwetse kusangalala kwa nkhope yanga.
25 Ndinawasankhira njira yao ndi kukhala mkulu wao.
Ndinakhala ngati mfumu mwa ankhondo ake,
ngati wotonthoza ofedwa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/29-61687a8946ef1c110c43364a7f10869e.mp3?version_id=1068—