1 Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo?
Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ake?
2 Alipo akusendeza malire;
alanda gulu la zoweta, nazidyetsa.
3 Akankhizira kwao bulu wa amasiye,
atenga ng’ombe ya mfedwa ikhale chikole.
4 Apatukitsa aumphawi m’njira;
osauka a padziko abisala pamodzi.
5 Taonani, ngati mbidzi za m’chipululu
atulukira kuntchito zao, nalawirira nkufuna chakudya;
chipululu chiwaonetsera chakudya cha ana ao.
6 Atema dzinthu zao m’munda;
natola khunkha m’munda wampesa wa woipa.
7 Agona amaliseche usiku wonse opanda chovala,
alibe chofunda pachisanu.
8 Avumbwa ndi mvula kumapiri,
nafukata thanthwe posowa pousapo.
9 Akwatula wamasiye kubere,
natenga chikole chovala cha osauka;
10 momwemo ayenda amaliseche opanda chovala,
nasenza mtolo wa dzinthu ali ndi njala.
11 M’kati mwa malinga a iwo aja ayenga mafuta;
aponda mphesa moponderamo, namva ludzu.
12 M’mzinda waukulu anthu abuula alinkufa;
ndi moyo wa iwo olasidwa ufuula;
koma Mulungu sasamalira choipacho.
13 Iwo ndiwo amene apikisana nako kuunika,
sadziwa njira zake, Sasunga mayendedwe ake.
14 Kukacha auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi;
ndi usiku asanduka mbala.
15 Ndipo diso la wachigololo liyembekezera chisisira,
ndi kuti, Palibe diso lidzandiona;
navala chophimba pankhope pake.
16 Kuli mdima aboola nyumba,
usana adzitsekera,
osadziwa kuunika.
17 Pakuti iwo onse auyesa m’mawa mthunzi wa imfa;
pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa.
18 Atengedwa ngati choyandama pamadzi;
gawo lao litembereredwa padziko;
sadzalunjikanso njira ya minda yampesa.
19 Chilala ndi dzuwa zitha madzi a chipale chofewa,
momwemo manda achita nao ochimwa.
20 M’mimba mudzamuiwala;
mphutsi zidzamudya mokondwera.
Sadzamkumbukiranso;
ndipo chosalungama chidzathyoledwa ngati mtengo.
21 Alusira chumba wosabala,
osamchitira wamasiye chokoma.
22 Mulungu awakhalitsa amphamvu mwa mphamvu yake;
iwo aukanso m’mene anayesa kuti sadzakhala ndi moyo.
23 Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo;
koma maso ake ali panjira zao.
24 Akwezeka; m’kamphindi kuli zii;
inde atsitsidwa, achotsedwa monga ena onse,
adulidwa ngati tirigu ngala zake.
25 Ndipo ngati si kutero, anditsutsa ndani kuti ndili wabodza,
ndi kuyesa mau anga opanda pake?
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/24-0ebef2528ceab784f33c50d5003ebd31.mp3?version_id=1068—