Yobu abwereza kukana kuti sanachimwe. Mulungu wosadziwika achita chifuniro chake. Kwambiri ochimwa oyenera kulangidwa akhala bwino m’moyo uno
1 Koma Yobu anayankha, nati,
2 Lero lomwe kudandaula kwanga kumawawa;
kulanga kwanga kuposa kubuula kwanga m’kulemera kwake.
3 Ha! Ndikadadziwa kumene ndikampeza Mulungu,
kuti ndifike kumpando wake!
4 Ndikadalongosola mlandu wanga pamaso pake,
ndikadadzaza m’kamwa mwanga ndi matsutsano.
5 Ndikadadziwa mau akadandiyankha ine,
ndikadazindikira chimene akadanena nane.
6 Akadatsutsana nane kodi mwa mphamvu yake yaikulu?
Iai, koma akadanditcherera khutu.
7 Apo woongoka mtima akadatsutsana naye;
ndipo ndikadapulumuka chipulumukire kwa Woweruza wanga.
8 Taonani, ndikanka m’tsogolo, kulibe Iye;
kapena m’mbuyo sindimzindikira;
9 akachita Iye kulamanzere, sindimpenyerera;
akabisala kulamanja, sindimuona.
10 Koma adziwa njira ndilowayi;
atandiyesa ndidzatuluka ngati golide.
11 Phazi langa lagwiratu moponda Iye,
ndasunga njira yake, wosapatukamo.
12 Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake;
ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga.
13 Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani?
Ndi ichi chimene moyo wake uchifuna achichita.
14 Pakuti adzachita chondiikidwiratu;
ndipo zambiri zotere zili ndi Iye.
15 Chifukwa chake ndiopsedwa pankhope pake;
ndikalingirira, ndichita mantha ndi Iye.
16 Pakuti Mulungu walefula mtima wanga,
ndi Wamphamvuyonse wandiopsa.
17 Popeza sindinalikhidwa usanafike mdimawo,
ndipo sanandiphimbire nkhope yanga ndi mdima wa bii.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/23-19fdf6c1cbf04aed83d4155c5d4aa7c3.mp3?version_id=1068—