Elifazi atsutsa Yobu pa kudzikuza kwake. Akuti, akulu omwe atsimikiza kuti ochimwa sakhala bwino
1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,
2 Kodi mwini nzeru ayankhe ndi kudziwa kouluzika,
ndi kudzaza mimba yake ndi mphepo ya kum’mawa?
3 Kodi atsutsane ndi mnzake ndi mau akusathandiza?
Kapena ndi maneno akusapindulitsa?
4 Zedi uyesa chabe mantha,
nuchepsa chilingiriro pamaso pa Mulungu.
5 Pakuti pakamwa pako paphunzitsa mphulupulu zako,
nusankha lilime la ochenjerera.
6 Pakamwa pako pakutsutsa, si ine ai.
Inde milomo yako ikuchitira umboni wakukutsutsa.
7 Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa?
Kapena unayamba kulengedwa ndiwe, osati mapiri?
8 Kodi unamva uphungu wachinsinsi wa Mulungu?
Ndipo unadzikokera nzeru kodi?
9 Udziwa chiyani, osachidziwa ife?
Uzindikira chiyani, chosakhala mwa ife?
10 Pakati pa ife pali aimvi, ndi okalambitsa,
akuposa atate wako masiku ao.
11 Masangalatso a Mulungu akuchepera kodi?
Kapena uli nacho chinsinsi kodi?
12 Mtima wako usonthokeranji nawe?
Maso ako aphethiraphethira chifukwa ninji?
13 Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu,
ndi kulola mau otere atuluke m’kamwa mwako.
14 Munthu nchiyani kuti akhale woyera,
wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?
15 Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ake;
ngakhale m’mwamba simuyera pamaso pake.
16 Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa,
wakumwa chosalungama ngati madzi.
17 Ndidzakuonetsa, undimvere;
chimene ndinachiona, ndidzakufotokozera;
18 chimene adachinena anzeru,
adachilandira kwa makolo ao, osachibisa;
19 ndiwo amene analandira okha dzikoli,
wosapita mlendo pakati pao.
20 Munthu woipa adzipweteka masiku ake onse,
ndi zaka zowerengeka zisingikira woopsa.
21 M’makutu mwake mumveka zoopsetsa;
pali mtendere amfikira wakumuononga.
22 Sakhulupirira kuti adzatulukamo mumdima,
koma kuti lupanga limlindira.
23 Ayendayenda ndi kufuna chakudya, nati, Chilikuti?
Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima.
24 Nsautso ndi chipsinjo zimchititsa mantha,
zimgonjetsa ngati mfumu yokonzekeratu kunkhondo.
25 Pakuti amtambasula dzanja lake moyambana ndi Mulungu,
napikisana ndi Wamphamvuyonse.
26 Amthamangira Iye mwaliuma,
ndi zikopa zake zochindikira.
27 Popeza anakuta nkhope yake ndi kunenepa kwake,
nachita mafunyenye a mafuta m’zuuno zake;
28 adzakhala m’mizinda yopasuka,
m’nyumba zosakhalamo munthu,
zoti zisandulika muunda.
29 Sadzakhala wolemera, ndi chuma chake sichidzakhalitsa,
ndi zipatso zake sizidzachuluka padziko.
30 Sadzachoka mumdima;
lawi la moto lidzaumitsa nthambi zake;
ndipo adzachoka ndi mpumo wa m’kamwa mwake.
31 Asatame zopanda pake, kudzinyenga nazo;
pakuti zopanda pake zidzakhala chombwezera chake.
32 Chidzachitika isanadze nthawi yake;
pakuti nthambi yake siidzaphuka.
33 Adzayoyoka zipatso zake zosapsa ngati mpesa,
nadzathothoka maluwa ake ngati mtengo waazitona.
34 Pakuti msonkhano wa onyoza Mulungu udzakhala chumba,
ndi moto udzapsereza mahema a olandira chokometsera mlandu.
35 Aima ndi chovuta, nabala mphulupulu,
ndi m’mimba mwao mukonzeratu chinyengo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/15-055e69e0a0493deaf497831e7675052e.mp3?version_id=1068—