Categories
YOBU

YOBU 14

1 Munthu wobadwa ndi mkazi

ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.

2 Atuluka ngati duwa, nafota;

athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.

3 Ndipo kodi mumtsegulira maso anu wotereyo,

ndi kunditenga kunena nane mlandu Inu?

4 Adzatulutsa choyera m’chinthu chodetsa ndani?

Nnena mmodzi yense.

5 Popeza masiku ake alembedwa,

chiwerengo cha miyezi yake chikhala ndi Inu,

ndipo mwamlembera malire ake kuti asapitirirepo iye;

6 mumleke osamthira maso, kuti apumule,

kuti akondwere nalo tsiku lake monga wolembedwa ntchito.

7 Pakuti akaulikha mtengo pali chiyembekezo kuti udzaphukanso,

ndi kuti nthambi yake yanthete siidzasowa.

8 Ngakhale muzu wake wakalamba m’nthaka,

ndi tsinde lake likufa pansi.

9 Koma pa mnunkho wa madzi udzaphuka,

nudzaswa nthambi ngati womera.

10 Koma munthu akufa atachita liondeonde

inde, munthu apereka mzimu wake, ndipo ali kuti?

11 Madzi achoka m’nyanja,

ndi mtsinje ukuphwa, nuuma;

12 momwemo munthu agona pansi, osaukanso;

kufikira miyamba kulibe, sadzaukanso,

kapena kuutsidwa pa tulo take.

13 Ha? Mukadandibisa kumanda,

mukadandisunga m’tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu.

Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.

14 Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?

Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga,

mpaka kwafika kusandulika kwanga.

15 Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani;

mukadakhumba ntchito ya manja anu.

16 Koma tsopano muwerenga moponda mwanga;

kodi simuyang’anitsa tchimo langa?

17 Cholakwa changa chaikidwa m’thumba lokhomedwa chizindikiro;

ndipo mumanga pamodzi mphulupulu zanga.

18 Ndipo zoonadi, likagwa phiri, latha;

ndi thanthwe lisunthika m’malo mwake.

19 Madzi anyenya miyala;

zosefukira zao zikokolola fumbi la nthaka;

ndipo muononga chiyembekezo cha munthu.

20 Mumpambana kotheratu, napita iye;

musintha nkhope yake, mumuuza achoke.

21 Ana ake aona ulemu osadziwa iye;

napeputsidwa, koma osazindikira za iwo.

22 Koma thupi lake limuwawira yekha,

ndi mtima wake umliritsa yekha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/14-05bb4dcdc6001c5feb27e4be78431419.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *