Categories
YOBU

YOBU 13

1 Taonani, diso langa lachiona chonsechi;

m’khutu mwanga ndachimva ndi kuchizindikira.

2 Chimene muchidziwa inu, inenso ndichidziwa;

sindikucheperani.

3 Koma ine ndidzanena ndi Wamphamvuyonse,

ndipo ndifuna kudzikanira kwa Mulungu.

4 Koma inu ndinu opanga zabodza,

asing’anga opanda pake inu nonse.

5 Mwenzi mutakhala chete konse,

ndiko kukadakhala nzeru zanu.

6 Tamvani tsono kudzikanira kwanga,

tamverani kudzinenera kwa milomo yanga.

7 Kodi munenera Mulungu mosalungama,

ndi kumnenera Iye monyenga?

8 Kodi mukhalira kumodzi ndi Iye?

Kodi mungamuimilire Mulungu pa mlandu?

9 Nchokoma kodi kuti Iye akusanthuleni?

Kodi mudzamnyenga Iye monga munyenga munthu?

10 Adzakudzudzulani ndithu,

mukachita tsankho m’tseri.

11 Ukulu wake sukuchititsani mantha,

ndi kuopsa kwake sikukugwerani kodi?

12 Zikumbutso zanu ndizo miyambi ya mapulusa;

zodzikanira zanu zikunga malinga adothi.

13 Khalani chete, ndilekeni, kuti ndinene,

chondifikira chifike.

14 Ndilumirenji mnofu wanga pamano panga,

ndi kupereka moyo wanga m’dzanja langa?

15 Angakhale andipha koma ndidzamlindira;

komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pake.

16 Iye adzakhalanso chipulumutso changa,

pakuti wonyoza Mulungu sadzafika pamaso pake.

17 Mvetsetsani mau anga,

ndi kunenetsa kwanga kumveke m’makutu mwanu.

18 Taonani tsono, ndalongosola mlandu wanga;

ndidziwa kuti adzandimasula ndili wolungama.

19 Ndaniyo adzatsutsana nane?

Ndikakhala chete, ndidzapereka mzimu wanga.

20 Zinthu ziwiri zokha musandichitire,

pamenepo sindidzabisalira nkhope yanu.

21 Mundichotsere dzanja lanu kutali,

ndi kuopsa kwanu kusandichititse mantha.

22 Pamenepo muitane, ndipo ndidzayankha;

kapena ndinene ndine, ndipo mundiyankhe ndinu.

23 Mphulupulu zanga ndi zochimwa zanga ndi zingati?

Mundidziwitse kulakwa kwanga ndi tchimo langa.

24 Mubisiranji nkhope yanu,

ndi kundiyesa mdani wanu?

25 Kodi mudzaopsa tsamba lakungouluka,

ndi kulondola ziputu zouma?

26 Pakuti mundilembera zinthu zowawa,

ndi kundipatsa ngati cholowa mphulupulu za ubwana wanga.

27 Mulonganso mapazi anga m’zigologolo,

ndi kupenyerera mayendedwe anga onse;

mudzilembera malire mopanika mapazi anga.

28 Momwemo munthu akutha ngati chinthu choola,

ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/13-ff29d48737c0c4e2fe0efe0563e5ffcb.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *