Categories
YOBU

YOBU 11

Zofari adzudzula Yobu pa kudzilungamitsa kwake, namchenjeza alape

1 Pamenepo anayankha Zofari wa ku Naama, nati,

2 Kodi mau ochulukawa sayenera kuwayankha?

Ndi munthu wa milomo ayenera kuyesedwa wolungama?

3 Kodi zotamanda zako ziwatseke anthu pakamwa?

Useka kodi, wopanda munthu wakukuchititsapo manyazi?

4 Pakuti unena, Chiphunzitso changa nchoona,

ndipo ndili woyera pamaso pako.

5 Koma, ha? Mwenzi atanena Mulungu,

ndi kukutsegulira milomo yake motsutsa;

6 nakufotokozere zinsinsi za nzeru,

popeza zipindikapindika machitidwe ao!

Chifukwa chake dziwa kuti Mulungu akuiwalira mphulupulu zina.

7 Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa mufunafuna?

Ukhoza kupeza Wamphamvuyonse motsindika?

8 Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungachitenji?

Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji?

9 Muyeso wake utalikira utali wake wa dziko lapansi,

chitando chake chiposa cha nyanja.

10 Akapita, nakatsekera,

nakatulutsa bwalo la mlandu, adzamletsa ndani?

11 Pakuti adziwa anthu opanda pake,

napenyanso mphulupulu, ngakhale saisamalira.

12 Koma munthu wopanda pake asowa nzeru,

ngakhale munthu abadwa ngati mwanawabulu.

13 Ukakonzeratu mtima wako,

ndi kumtambasulira Iye manja ako;

14 Mukakhala mphulupulu m’dzanja lako, uichotseretu kutali,

ndi chisalungamo chisakhale m’mahema mwako.

15 Popeza pamenepo udzakweza nkhope yako opanda banga;

nudzalimbika osachita mantha;

16 pakuti udzaiwala chisoni chako,

udzachikumbukira ngati madzi opita.

17 Ndipo moyo wako udzayera koposa usana;

kungakhale kuli mdima kudzakhala ngati m’mawa.

18 Ndipo udzalimbika mtima popeza pali chiyembekezo;

nudzafunafuna, ndi kugona mosatekeseka.

19 Inde udzagona pansi, wopanda wina wakukunjenjemeretsa,

ndipo ambiri adzakupembedza.

20 Koma maso a oipa adzagoma,

ndi pothawirapo padzawasowa,

ndipo chiyembekezo chao ndicho kupereka mzimu wao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/11-26d69c25d7343eef21a294904e13e96c.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *