Kupembedza mafano kwa Israele
1 Wolungama atayika, ndipo palibe munthu wosamalirapo; ndipo anthu achifundo atengedwa, palibe wolingalira kuti wolungama achotsedwa pa choipa chilinkudza.
2 Iye alowa mumtendere, iwo apuma pa mphasa zao, yense woyenda moongoka.
3 Koma sendererani kuno chifupi, inu ana aamuna a watsenga, mbeu yachigololo ndi yadama.
4 Ndiye yani mudzikondweretsa momseka? Ndani mulikumyasamira kukamwa, ndi kumtulutsira lilime? Kodi inu simuli ana akulakwa, mbeu yonama?
5 Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m’zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?
6 Pakuti pa miyala yosalala ya m’chigwa pali gawo lako; iyo ndiyo gawo lako; ndiyo imene unaitsanulirira nsembe yothira, ndi kupereka nsembe yaufa. Kodi ndidzapembedzedwa pa zinthu zimenezi?
7 Pamwamba paphiri lalitalitali unayala mphasa yako; kumenekonso wakwera kukapereka nsembe.
8 Ndi kumbuyo kwa zitseko ndi mphuthu waimiritsa chikumbutso chako, pakuti wadzionetsa wekha kwa wina, wosati kwa Ine; ndipo wakwerako, wakuza mphasa yako, ndi kupangana nao pangano; unakonda mphasa yao kumene unaiona.
9 Ndipo unanka kwa mfumu, utadzola mafuta ndi kuchulukitsa zonunkhira zako; ndipo unatumiza atumwi ako kutali; ndipo wadzichepetsa wekha kufikira kunsi kumanda.
10 Unatopa ndi njira yako yaitali; koma sunanene, Palibe chiyembekezo; iwe wapeza moyo wa dzanja lako; chifukwa chake sunalefuke.
11 Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kuchita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhale chete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiope Ine konse?
12 Ndidzaonetsa chilungamo chako ndi ntchito zako sudzapindula nazo.
13 Pamene pakufuula iwe akupulumutse amene unawasonkhanitsa; koma mphepo idzawatenga, mpweya udzachotsa onse; koma iye amene andikhulupirira Ine adzakhala ndi dziko, nadzakhala nacho cholowa m’phiri langa lopatulika.
14 Ndipo adzanena, Undani, undani, konzani njira, chotsani chokhumudwitsa m’njira mwa anthu anga.
15 Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m’malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
16 Pakuti sindidzatsutsana kunthawi zonse, sindidzakwiya masiku onse; pakuti mzimu udzalefuka pamaso pa Ine, ndi miyoyo imene ndinailenga.
17 Chifukwa cha kuipa kwa kusirira kwake ndinakwiya ndi kummenya iye; ndinabisa nkhope yanga, ndipo ndinakwiya; ndipo iye anankabe mokhota m’njira ya mtima wake.
18 Ndaona njira zake, ndipo ndidzamchiritsa; ndidzamtsogoleranso, ndi kumbwezera iye ndi olira maliro ake zotonthoza mtima.
19 Ndilenga chipatso cha milomo, Mtendere, mtendere kwa iye amene ali kutali, ndi kwa iye amene ali chifupi, ati Yehova; ndipo ndidzamchiritsa iye.
20 Koma oipa ali ofanana ndi nyanja yowinduka; pakuti siingapume, ndi madzi ake autsa matope ndi uve.
21 Palibe mtendere, ati Mulungu wanga, kwa oipa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/57-5b0a6bc0d892276f830d23a061567e69.mp3?version_id=1068—