Categories
YESAYA

YESAYA 56

Malonjezo a kwa iwo osunga Sabata

1 Atero Yehova, Sungani inu chiweruziro, ndi kuchita chilungamo; pakuti chipulumutso changa chili pafupi kudza, ndi chilungamo changa chili pafupi kuti chivumbulutsidwe.

2 Wodala munthu amene achita ichi, ndi mwana wa munthu amene agwira zolimba ichi, amene asungaSabataosaliipitsa, nasunga dzanja lake osachita nalo choipa chilichonse.

3 Mlendo amene wadziphatika yekha kwa Yehova asanene, kuti, Yehova adzandilekanitsa ndithu ndi anthu ake; pena mfule asanene, Taonani ine ndili mtengo wouma.

4 Pakuti atero Yehova kwa mifule imene isunga masabata, nisankha zinthu zimene zindikondweretsa Ine, nigwira zolimbachipanganochanga,

5 Kwa iyo ndidzapatsa m’nyumba yanga ndi m’kati mwa makoma anga malo, ndi dzina loposa la ana aamuna ndi aakazi; ndidzawapatsa dzina lachikhalire limene silidzadulidwa.

6 Alendonso amene adziphatika okha kwa Yehova, kuti amtumikire Iye, ndi kukonda dzina la Yehova, akhale atumiki ake, yense amene asunga sabata osaliipitsa, nagwira zolimba chipangano changa;

7 naonso ndidzanka nao kuphiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m’nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zao zopsereza ndi nsembe zao zidzalandiridwa paguwa langa la nsembe; pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.

8 Ambuye Yehova amene asonkhanitsa otayika a Israele ati, Komabe ndidzasonkhanitsa ena kwa iye, pamodzi ndi osonkhanitsidwa akeake.

9 Inu zilombo zonse za m’thengo, idzani kulusa, inde zilombo inu nonse za m’nkhalango.

10 Alonda ake ali akhungu, iwo onse ali opanda nzeru; iwo onse ali agalu achete, osatha kuuwa; kungolota, kugona pansi, kukonda kugona tulo.

11 Inde agalu ali osusuka, sakhuta konse; amenewa ali abusa osazindikira; iwo onse atembenukira kunjira zao, yense kutsata phindu lake m’dera lake.

12 Idzani inu, ati iwo, ndidzatengera vinyo, ndipo tidzakhuta chakumwa chaukali; ndipo mawa kudzakhala monga tsiku lalero, tsiku lalikulu loposa ndithu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/56-653943d7addeab577a82b3e5caf6fd0f.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *