Categories
YESAYA

YESAYA 55

Osauka onse aitanidwa alandire chipulumutso

1 Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osowa ndalama idzani inu mugule mudye; inde idzani, mugule vinyo ndi mkaka opanda ndalama ndi opanda mtengo wake.

2 Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.

3 Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanuchipanganochosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.

4 Taonani, ndampereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu.

5 Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwe, ndi mtundu umene sunakudziwe udzakuthamangira, chifukwa cha Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele; pakuti Iye wakukometsa.

6 Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi;

7 woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.

8 Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu sizili njira zanga, ati Yehova.

9 Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.

10 Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya;

11 momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m’mene ndinawatumizira.

12 Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m’thengo idzaomba m’manja mwao.

13 M’malo mwa mithethe mudzatuluka mtengo wamlombwa; ndi m’malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamchisu; ndipo chidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati chizindikiro chosatha, chimene sichidzalikhidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/55-658b0c9676ccf9765588567f90f3c3b9.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *