Categories
YESAYA

YESAYA 54

Zokoma zimene Yehova adzachitira Mpingo wao

1 Imba, iwe wouma, amene sunabale; imba zolimba ndi kufuula zolimba, iwe amene sunabale mwana; pakuti ana a mfedwa achuluka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.

2 Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.

3 Pakuti iwe udzafalikira ponse padzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbeu yako idzalandiraamitunducholowa chao, ndi kukhalitsa anthu m’mabwinja.

4 Usaope, pakuti sudzakhala ndi manyazi; usasokonezedwe, pakuti sudzachitidwa manyazi; pakuti udzaiwala manyazi a ubwana wako, ndi chitonzo cha umasiye wako sudzachikumbukiranso.

5 Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.

6 Pakuti Yehova wakuitana iwe monga mkazi wakusiyidwa ndi wosauka m’mzimu, ngakhale mkazi wa ubwana wochotsedwa, ati Mulungu wako.

7 Kamphindi kakang’ono ndakusiya iwe, koma ndi chifundo chambiri ndidzakusonkhanitsa.

8 M’kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa chikhalire ndidzakuchitira chifundo, ati Yehova Mombolo wako.

9 Pakuti kumeneku kuli kwa Ine monga madzi a Nowa; pakuti monga ndinalumbira kuti madzi a Nowa sadzamizanso padziko lapansi, momwemo ndinalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe, pena kukudzudzula.

10 Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthikachipanganochanga cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.

11 Iwe wosautsidwa, wobelukabeluka ndi namondwe, wosatonthola mtima, taona, ndidzakhazika miyala yako m’mawangamawanga abwino, ndi kukhazika maziko ako ndi masafiro.

12 Ndipo ndidzamanga mazenera ako ndi miyala yofiira, ndi zipata zako ndi bareketi, ndi malire ako onse ndi miyala yokondweretsa.

13 Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.

14 M’chilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutali ndi chipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutali ndi mantha, pakuti sadzafika chifupi ndi iwe.

15 Taona, iwo angasonkhanitse pamodzi, koma si ndi Ine; aliyense amene adzasonkhana pamodzi akangane ndi iwe adzagwa chifukwa cha iwe.

16 Taona, ndalenga wachipala amene avukuta moto wamakala, ndi kutulutsamo chida cha ntchito yake; ndipo ndalenga woononga kuti apasule.

17 Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m’chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/54-5210c587531122fc23220f92ac31b251.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *