Categories
YESAYA

YESAYA 53

Masomphenya a chisauko ndi ulemerero wa Mtumiki wa Yehova

1 Ndani wamvera uthenga wathu? Ndi mkono wa Yehova wavumbulukira yani?

2 Pakuti ameneyo adzaphuka pamaso pake ngati mtengo wanthete, ndi ngati muzu womera m’nthaka youma; Iye alibe maonekedwe, pena kukongola; ndipo pamene timuona palibe kukongola kuti timkhumbe.

3 Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.

4 Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuyesa wokhomedwa, wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wovutidwa.

5 Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.

6 Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m’njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.

7 Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngatimwanawankhosaamene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake.

8 Anachotsedwa ku chipsinjo ndi chiweruziro; ndipo ndani adzafotokoza nthawi ya moyo wake? Pakuti walikhidwa kunja kuno; chifukwa cha kulakwa kwa anthu anga Iye anakhomedwa.

9 Ndipo anaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yake, ngakhale Iye sanachite chiwawa, ndipo m’kamwa mwake munalibe chinyengo.

10 Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m’manja mwake.

11 Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.

12 Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/53-5f7368a53cc8f5ace9d9ae84f8510530.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *