1 Galamuka! Galamuka! Tavala mphamvu zako,Ziyoni; tavala zovala zako zokongola,Yerusalemu, mzinda wopatulika; pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso kwa iwe wosadulidwa ndi wodetsedwa.
2 Dzisanse fumbi; uka, khala tsonga, Yerusalemu; udzimasulire maunyolo a pakhosi pako, iwe mwana wamkazi wam’nsinga wa Ziyoni.
3 Pakuti atero Yehova, Inu munagulitsidwa chabe, ndipo mudzaomboledwa opanda ndalama.
4 Pakuti Ambuye Yehova atero, Anthu anga ananka ku Ejipito poyamba paja, kukakhala kumeneko; ndipo Asiriya anawatsendereza popanda chifukwa.
5 Chifukwa chake kodi ndichitenji pano? Ati Yehova; popeza anthu anga achotsedwa popanda kanthu? Akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa lichitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza.
6 Chifukwa chake anthu anga adzadziwa dzina langa; chifukwa chake tsiku limenelo iwo adzadziwa kuti Ine ndine amene ndinena; taonani, ndine pano.
7 Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.
8 Mau a alonda ako! Akweza mau, aimba pamodzi; pakuti adzaona maso ndi maso, pamene Yehova abwerera kudza ku Ziyoni.
9 Kondwani zolimba, imbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, waombola Yerusalemu.
10 Yehova wavula mkono wake woyera pamaso paamitunduonse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
11 Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.
12 Pakuti simudzachoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israele adzadikira pambuyo panu.
13 Taonani, Mtumiki wanga adzachita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba.
14 Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israele, momwemo nkhope yake yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu aliyense, ndi maonekedwe ake kupambana ana a anthu;
15 momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwe kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/52-f9ff7d4f82f04bbfdadf894087c9d81b.mp3?version_id=1068—