Mtumiki wa Yehova anyozedwa koma athandizidwa
1 Atero Yehova, Kalata ya chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.
2 Chifukwa chanji ndinafika osapeza munthu? Ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? Pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndi kusandutsa mitsinje chipululu; nsomba zake zinunkha chifukwa mulibe madzi, ndipo zifa ndi ludzu.
3 Ndiveka thambo ndi kuda, ndi kuyesa chiguduli chofunda chake.
4 Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m’mawa ndi m’mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.
5 Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhale wopanduka ngakhale kubwerera m’mbuyo.
6 Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisire nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.
7 Pakuti Ambuye Yehova adzandithangata Ine; chifukwa chake sindinasokonezedwa; chifukwa chake ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndidziwa kuti sindidzakhala ndi manyazi.
8 Iye ali pafupi amene alungamitsa Ine; ndani adzakangana ndi Ine? Tiyeni tiimirire tonse pamodzi; mdani wanga ndani? Andiyandikire.
9 Taonani, Ambuye Yehova adzathandiza Ine; ndani amene adzanditsutsa? Taonani, iwo onse adzatha ngati chovala, njenjete zidzawadya.
10 Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.
11 Taonani, inu nonse amene muyatsa moto, amene mudzimangira m’chuuno ndi nsakali, yendani inu m’chilangali cha moto wanu, ndi pakati pa nsakali zimene mwaziyatsa. Ichi mudzakhala nacho cha padzanja langa; mudzagona pansi ndi chisoni.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/50-23a365c473f4f6ce2a6095fec4ea226d.mp3?version_id=1068—