Categories
YESAYA

YESAYA 48

Awadandaulira Aisraele, awachenjeza, nalonjezana nao

1 Imvani inu ichi, banja la Yakobo, amene mutchedwa ndi dzina la Israele, amene munatuluka m’madzi a Yuda amene mulumbira dzina la Yehova ndi kutchula dzina la Mulungu wa Israele, koma si m’zoona, pena m’chilungamo.

2 Pakuti adziyesa okha a mzinda wopatulika, ndi kudzikhazikitsa iwo okha pa Mulungu wa Israele; dzina lake ndi Yehova wa makamu.

3 Ndanena zinthu zoyamba kuyambira kale; inde, izo zinatuluka m’kamwa mwanga, ndipo ndinazisonyeza; mwadzidzidzi ndinazichita izo, ndipo zinaoneka.

4 Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako lili mtsempha wachitsulo, ndi mphumi yako mkuwa;

5 chifukwa chake ndinakudziwitsa ichi kuyambira kale; chisanaoneke ndinakusonyeza icho, kuti iwe unganene, Fano langa lachita izo, ndi chifaniziro changa chosema, ndi chifaniziro changa choyenga zinazilamulira.

6 Iwe wachimva; taona zonsezi; ndipo inu kodi inu simudzachinena? Ndakusonyeza iwe zinthu zatsopano kuchokera nthawi ino, ngakhale zinthu zobisika, zimene iwe sunazidziwe.

7 Zalengedwa tsopano, zosati kuyambira kale; ndipo lisanafike tsiku laleroli iwe sunazimve; unganene, Taonani, ndinazidziwa.

8 Inde, iwe sunamve; inde, sunadziwe; inde kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wachita mwachiwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa chibadwire.

9 Chifukwa cha dzina langa ndidzachedwetsa mkwiyo wanga, ndi chifukwa cha kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakuchotse.

10 Taona ndakuyenga, koma si mongasiliva, ndakuyesa iwe m’ng’anjo ya masautso.

11 Chifukwa cha Ine ndekha, chifukwa cha Ine ndekha ndidzachita ichi, pakuti dzina langa lidetsedwerenji? Ndi ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina.

12 Mverani Ine, Yakobo ndi Israele, oitanidwa anga, Ine ndine; ndine woyamba, Inenso ndine womaliza.

13 Inde dzanja langa linakhazika maziko a dziko lapansi, ndi dzanja langa lamanja linafunyulula m’mwamba; pakuziitana Ine ziimirira pamodzi.

14 Sonkhanani inu nonse ndi kumva, ndani mwa iwo aonetsa zinthu izi? Iye amene Yehova anamkonda, iye adzachita kufuna kwake pa Babiloni, ndi mkono wake udzakhala pa Ababiloni.

15 Ine, ngakhale Ine ndanena; inde ndamwitana iye, ndamfikitsa, ndipo adzapindula nayo njira yake.

16 Idzani inu chifupi ndi Ine, imvani ichi; kuyambira pa chiyambi sindinanene m’tseri; chiyambire zimenezi, Ine ndilipo; ndipo tsopano Ambuye Mulungu wanditumiza Ine ndi mzimu wake.

17 Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.

18 Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja;

19 mbeu yakonso ikadakhala monga mchenga, ndi obadwa a m’chuuno mwako momwemo; dzina lake silikadachotsedwa, pena kuonongeka pamaso panga.

20 Tulukani inu mu Babiloni, athaweni Ababiloni; ndi mau akuimba nenani inu, bukitsani ichi, lalikirani ichi, ngakhale ku malekezero a dziko; nenani, Yehova waombola mtumiki wake Yakobo.

21 Ndipo iwo sanamve ludzu, pamene Iye anawatsogolera m’mapululu; anawatulutsira madzi kutuluka m’matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika.

22 Kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/48-91a7d481441172fbae83c7ff6fc9751e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *