Babiloni adzaonongeka konse
1 Tsika, ukhale m’fumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babiloni; khala pansi popanda mpando wachifumu, mwana wamkazi wa Ababiloni, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka.
2 Tenga mipero, nupere ufa; chotsa chophimba chako, vula chofunda, kwinda m’mwendo, oloka mitsinje.
3 Maliseche ako adzakhala osafundidwa, inde, manyazi ako adzaoneka; ndidzachita kubwezera, osasamalira munthu.
4 Mombolo wathu, Yehova wa makamu ndi dzina lake, Woyera wa Israele.
5 Khala iwe chete, lowa mumdima, mwana wamkazi wa Ababiloni; pakuti sudzatchedwanso mkazi wa maufumu.
6 Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa cholowa changa, ndi kuwapereka m’manja ako; koma iwe sunawaonetsere chifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.
7 Ndipo unati, Ndidzakhala mkazi wa mfumu wa nthawi zonse; ndipo sunasamalire izi mumtima mwako, kapena kukumbukira chomalizira chake.
8 Chifukwa chake tsono, imva ichi, iwe wotsata zokondweretsa, amene umakhala mosatekeseka, amene umati mumtima mwako, Ine ndine, ndipo popanda ine palibenso wina; sindidzakhala monga mkazi wamasiye, kapena kudziwa kumwalira kwa ana;
9 koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa maphenda ako ambirimbiri.
10 Pakuti wakhulupirira zoipa zako, wati, Palibe wondiona ine; nzeru zako ndi chidziwitso chako zakusandutsa woipa; ndipo wanena mumtima mwako, Ndine, ndipo popanda ine palibenso wina.
11 Chifukwa chake choipa chidzafika pa iwe; sudzadziwa kucha kwake, ndipo chionongeko chidzakugwera; sudzatha kuchikankhira kumbali; ndipo chipasuko chosachidziwa iwe chidzakugwera mwadzidzidzi.
12 Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m’menemo iwe unagwira ntchito chiyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.
13 Watopa mu uphungu wako wambiri; aimirire tsopano openda zam’mwamba, oyang’ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi, ndi kukupulumutsa pa zinthu zimene zidzakugwera.
14 Taona, iwo adzakhala ngati ziputu, moto udzawatentha iwo; sadzadzipulumutsa okha kumphamvu za malawi; motowo sudzakhala khala loothako, pena moto wakukhalako.
15 Zinthu zomwe unagwira ntchito yake, zidzatero nawe; iwo amene anachita malonda ndi iwe chiyambire pa ubwana wako, adzayenda yense kunka kumalo kwake; sipadzakhala wopulumutsa iwe.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/47-82ba4ef1b918cb4954434fd2c0c95ead.mp3?version_id=1068—