Categories
YESAYA

YESAYA 45

Yehova amuyesa Kirusi chipangizo chake

1 Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Kirusi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, ndipo ndidzamasula m’chuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pake, ndi zipata sizidzatsekedwa:

2 Ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzathyolathyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapichi achitsulo;

3 ndipo ndidzakupatsa iwe chuma cha mumdima, ndi zolemera zobisika za m’malo am’tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israele.

4 Ndakuitana iwe dzina lako, chifukwa cha Yakobo mtumiki wanga ndi Israele wosankhidwa wanga; ndakuonjezera dzina, ngakhale iwe sunandidziwe Ine.

5 Ine ndili Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m’chuuno, ngakhale sunandidziwe;

6 kuti anthu akadziwe kuchokera kumatulukiro a dzuwa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso.

7 Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.

8 Igwani pansi, inu m’mwamba, kuchokera kumwamba, thambo litsanulire pansi chilungamo; dziko lapansi litseguke, kuti libalitse chipulumutso, nilimeretse chilungamo chimere pamodzi; Ine Yehova ndinachilenga chimenecho.

9 Tsoka kwa iye amene akangana ndi Mlengi wake! Phale mwa mapale a dziko lapansi! Kodi dongo linganene kwa iye amene aliumba, Kodi upanga chiyani? Pena ntchito yako, Iye alibe manja?

10 Tsoka kwa iye amene ati kwa atate wake, Kodi iwe ubalanji? Pena kwa mkazi, Ulikusauka ninji iwe?

11 Atero Yehova Woyera wa Israele ndi Mlengi wake, Ndifunse Ine za zinthu zimene zilinkudza; za ana anga aamuna, ndi za ntchito ya manja anga, ndilamulireni Ine.

12 Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; Ine, ngakhale manja anga, ndafunyulula kumwamba, ndi zonse za m’menemo, ndinazilamulira ndine.

13 Ine ndautsa Kirusi m’chilungamo, ndipo ndidzalungamitsa njira zake zonse; iye adzamanga mzinda wanga, nadzaleka andende anga anke mwaufulu, wosati ndi mtengo pena mphotho, ati Yehova wa makamu.

14 Atero Yehova, Ntchito ya Ejipito, ndi malonda a Kusi, ndi a Seba, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m’maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.

15 Ndithu Inu ndinu Mulungu, amene mudzibisa nokha, Mulungu wa Israele, Mpulumutsi.

16 Iwo adzakhala ndi manyazi, inde, adzathedwa nzeru onsewo; adzalowa m’masokonezo pamodzi, amene apanga mafano.

17 Koma Israele adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi chipulumutso chosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru kunthawi zosatha.

18 Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenge mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.

19 Ine sindinanene m’tseri m’malo a dziko la mdima; Ine sindinati kwa mbeu ya Yakobo, Mundifune Ine mwachabe; Ine Yehova ndinena chilungamo, ndinena zimene zili zoona.

20 Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani chifupi pamodzi, inu amene mwapulumukaamitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mulungu wosakhoza kupulumutsa.

21 Nenani inu, tulutsani mlandu wanu; inde, achite uphungu pamodzi; ndani waonetsa ichi chiyambire nthawi yakale? Ndani wanena ichi kale? Kodi si ndine Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine.

22 Yang’anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko; pakuti Ine ndine Mulungu, palibe wina.

23 Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m’kamwa mwanga m’chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.

24 Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.

25 Mwa Yehova mbeu yonse ya Israele idzalungamitsidwa ndi kudzikuza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/45-7df87c22df3de720e9f77f354cfe3adf.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *