Categories
YESAYA

YESAYA 38

Kudwala kwa Hezekiya ndi kuchiritsidwa kwake

1 Masiku amenewo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Ndipo Yesayamneneri, mwana wa Amozi, anadza kwa iye, nati kwa iye, Atero Yehova, Konza nyumba yako, pakuti iwe udzafa, sudzakhala ndi moyo.

2 Ndipo Hezekiya analoza nkhope yake kukhoma, napemphera kwa Yehova, nati,

3 Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m’zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndachita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.

4 Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yesaya, ndi kuti,

5 Ukanene kwa Hezekiya, Atero Yehova, Mulungu wa Davide, kholo lako, Ndamva kupemphera kwako, ndaona misozi yako; taona, ndidzaonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu.

6 Ndipo ndidzakupulumutsa iwe ndi mzinda uno m’manja mwa mfumu ya Asiriya, ndipo ndidzatchinjiriza mzinda uno.

7 Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe chochokera kwa Yehova, kuti Yehova adzachita ichi wanenachi;

8 taona, ndidzabweza mthunzi wa pamakwerero, umene watsika pa makwerero a Ahazi ndi dzuwa, ubwerere makwerero khumi. Ndipo dzuwa linabwerera makwerero khumi pamakwerero, pamene udatsika mthunziwo.

9 Malemba a Hezekiya mfumu ya Ayuda muja anadwala, atachira nthenda yake.

10 Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m’zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala.

11 Ndinati, Sindidzaona Yehova m’dziko la amoyo; sindidzaonanso munthu pamodzi ndi okhala kunja kuno;

12 Pokhala panga pachotsedwa, pandisunthikira monga hema wa mbusa; Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba; Iye adzandidula ine poomberapo; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.

13 Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anathyolathyola mafupa anga onse; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.

14 Ndinalankhulalankhula ngati namzeze, pena chumba; Ndinalira maliro ngati nkhunda; maso anga analephera pogadamira kumwamba. Ambuye ndasautsidwa, mundiperekere chikoli.

15 Kodi ndidzanena chiyani? Iye wanena kwa ine, ndiponso Iye mwini wachita ichi; Ine ndidzayenda chete zaka zanga zonse, chifukwa cha zowawa za moyo wanga.

16 Ambuye ndi zinthu izi anthu akhala ndi moyo. Ndipo m’menemo monse muli moyo wa mzimu wanga; Chifukwa chake mundichiritse ine, ndi kundikhalitsa ndi moyo.

17 Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m’dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m’mbuyo mwanu machimo anga onse.

18 Pakuti kunsi kwa manda sikungakuyamikeni Inu; imfa singakulemekezeni; Otsikira kudzenje sangaziyembekeze zoona zanu.

19 Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.

20 Yehova ndiye wondipulumutsa ine; Chifukwa chake tidzaimba nyimbo zanga, ndi zoimba zazingwe Masiku onse a moyo wathu m’nyumba ya Yehova.

21 Ndipo Yesaya adati, Atenge m’bulu wankhuyu, auike pafundo, ndipo iye adzachira.

22 Hezekiya anatinso, Chizindikiro nchiyani, kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/38-77634b85d007fba63ddbfdf6d0dffc03.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *