Categories
YESAYA

YESAYA 35

Chikondwerero cha Ziyoni m’tsogolomo

1 Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti see lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa.

2 Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni, ndi ukulu wa Karimele ndi Saroni; anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu.

3 Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo a gwedegwede.

4 Nenani kwa a mitima ya chinthenthe, Limbani, musaope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera chilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani.

5 Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa.

6 Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti see.

7 Ndipo mchenga wong’azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m’malo a ankhandwe m’mene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.

8 Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa njira yopatulika; odetsedwa sadzapita m’menemo; koma Iye adzakhala nao oyenda m’njira, ngakhale opusa, sadzasochera m’menemo.

9 Sikudzakhala mkango kumeneko, ngakhale chilombo cholusa sichidzapondapo, pena kupezedwa pamenepo; koma akuomboledwa adzayenda m’menemo;

10 ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika kuZiyonialikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/35-6c7b4e6a935ed6f4bd440bc4d2cc5726.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *