Categories
YESAYA

YESAYA 32

Ufumu wa mfumu yolungama

1 Taonani mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo.

2 Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.

3 Ndipo maso a iwo amene aona sadzatsinzina, ndi makutu a iwo amene amva adzamvera.

4 Mtimanso wansontho udzadziwa nzeru, ndi lilime la achibwibwi lidzalankhula zomveka msanga.

5 Wopusa sadzayesedwanso woolowa manja, ngakhale wouma manja sadzayesedwa mfulu.

6 Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.

7 Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.

8 Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m’zaufulu zomwe.

Chilangizo cha kwa akazi

9 Ukani, akazi inu, amene mulinkukhala phee, mumve mau anga; inu ana aakazi osasamalira, tcherani makutu pa kulankhula kwanga.

10 Pakutha chaka, kudza masiku ena inu mudzavutidwa, inu akazi osasamalira; pakuti masika a mphesa adzasoweka, sadzatuta konse.

11 Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhala phee; vutidwani, inu osasamalira, vulani mukhale maliseche, nimumange chiguduli m’chuuno mwanu.

12 Iwo adzadzimenya pazifuwa chifukwa cha minda yabwino, chifukwa cha mpesa wobalitsa.

13 Padziko la anthu anga padzafika minga ndi lunguzi; inde pa nyumba zonse zokondwa, m’mzinda wokondwerera;

14 pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mzinda wa anthu ambiri udzakhala bwinja; chitunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba kunthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta;

15 kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kuchokera kumwamba, ndi chipululu chidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.

16 Pamenepo chiweruzo chidzakhala m’chipululu, ndi chilungamo chidzakhala m’munda wobalitsa.

17 Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.

18 Ndipo anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.

19 Koma kudzagwa matalala m’kugwa kwake kwa nkhalango; ndipo mzinda udzagwetsedwa ndithu.

20 Odala muli inu, amene mubzala m’mbali mwa madzi monse, amene muyendetsa mapazi a ng’ombe ndi bulu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/32-5dd9d762e3acebb5c428e1fdc188fe8c.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *