Categories
YESAYA

YESAYA 31

Tsoka otama chithandizo cha Ejipito

1 Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Ejipito kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magaleta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang’ana Woyera wa Israele, ngakhale kumfuna Yehova!

2 Koma Iyenso ndi wanzeru, nadzatengera choipa, ndipo sadzabwezanso mau ake, koma adzaukira banja la ochita zoipa, ndi amene athandiza iwo akugwira ntchito yoipa.

3 Koma Aejipito ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lake, wothandiza adzaphunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera.

4 Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yake, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupirikitsa, ngakhale kudzichepetsa wokha, chifukwa cha phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo kuphiri laZiyoni, ndi kuchitunda kwake komwe.

5 Monga mbalame ziuluka, motero Yehova wa makamu adzatchinjirizaYerusalemu; Iye adzatchinjirikiza ndi kuupulumutsa, adzapitirapo ndi kuusunga.

6 Bwerani kwa Iye amene mwampandukira kolimba, ana a Israele inu.

7 Pakuti tsiku limenelo iwo adzataya munthu yense mafano ake asiliva, ndi mafano ake agolide amene manja anuanu anawapanga akuchimwitseni inu.

8 Pamenepo Asiriya adzagwa ndi lupanga losati la munthu; ndi lupanga losati la anthu lidzammaliza iye; ndipo iye adzathawa lupanga, ndi anyamata ake adzalamba.

9 Ndipo mwala wake udzachoka, chifukwa cha mantha, ndi akalonga ake adzaopa mbendera, ati Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni, ndi ng’anjo yake mu Yerusalemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/31-eced3ee99deab8257740a8f7998265e1.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *