Aneneratu za kugwa kwa Babiloni
1 Katundu wa chipululu cha kunyanja. Monga akamvulumvulu a kumwera apitirira, kufumira kuchipululu kudziko loopsa.
2 Masomphenya ovuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Mediya iwe; kuusa moyo kwake konse ndakutonthoza.
3 Chifukwa chake m’chuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndichita mantha sindingathe kuona.
4 Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; chizirezire chimene ndinachikhumba chandisandukira kunthunthumira.
5 Iwo akonza pa gome lodyera, aika alonda, adya, namwa; ukani, akalonga inu, dzozani mafuta chikopa.
6 Pakuti Ambuye atero kwa ine, Muka, ika mlonda anene chimene achiona;
7 ndipo pamene iye anaona khamu, amuna apakavalo awiriawiri, khamu la abulu, khamu langamira, iye adzamvetsera ndi khama mosamalitsa.
8 Ndipo iye anafuulitsa ngati mkango, Ambuye inu, ine ndiimabe pamwamba pa nsanja nthawi ya usana, ndipo ndiikidwa mu ulonda wanga usiku wonse;
9 ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apakavalo awiriawiri. Ndipo iye anayankha nati, Babiloni wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yake asweka, nagwa pansi.
10 Kuomba kwanga nanga, ndi za pa dwale langa: chimene ine ndinachimva kwa Yehova wa makamu Mulungu wa Israele, ndanena kwa inu.
Aneneratu za kuonongeka kwa Duma
11 Katundu wa Duma. Wina aitana kwa ine kuchokera ku Seiri, Mlonda, nthawi yanji ya usiku? Mlonda, nthawi yanji ya usiku?
12 Mlonda anati, Kuli kucha, koma kukali usiku; mukafuna kufunsa, funsani, bwerani, idzani.
Za kuonongeka kwa Arabiya
13 Katundu wa pa Arabiya. M’nkhalango ya mu Arabiya mudzagona, inu makamu oyendayenda a Dedani.
14 Muchingamire akumva ludzu ndi madzi; okhala m’dziko la Tema ananka kukomana ndi othawa ndi chakudya chao.
15 Pakuti iwo anathawa malupanga, malupanga osololedwa, ndi mauta olifuka ndi nkhondo yovuta.
16 Pakuti Ambuye anatero kwa ine, Chisanapite chaka malinga ndi zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wonse wa Kedara udzagoma;
17 ndi otsala amauta, ngwazi za ana a Kedara zidzachepa, pakuti Yehova Mulungu wa Israele wanena.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/21-e8c016b132491e62a698be6420815038.mp3?version_id=1068—