Categories
YESAYA

YESAYA 13

Aneneratu za kuthyoka kwa ufumu wa Babiloni, ndi kubweza Israele kwao

1 Katundu wa Babiloni, amene anamuona Yesaya mwana wa Amozi.

2 Kwezani mbendera paphiri loti see, kwezani mau kwa iwo, kodolani kuti alowe m’zipata za akulu.

3 Ine ndalamulira opatulidwa anga, inde, ndaitana amphamvu anga, achite mkwiyo wanga, okondwerera ndi ukulu wanga.

4 Mau a khamu m’mapiri, akunga a mtundu waukulu wa anthu, mau a phokoso la maufumu a mitundu yosonkhanidwa! Yehova wa makamu asonkhanitsa khamu kunkhondo.

5 Achokera m’dziko lakutali, kumalekezero a thambo, ngakhale Yehova, ndi zida za mkwiyo wake, kuti aononge dziko lonse.

6 Kuwani inu; pakuti tsiku la Yehova lili pafupi; lidzafika monga chionongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.

7 Chifukwa chake manja onse adzafooka, ndi mitima yonse ya anthu idzasungunuka;

8 ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto.

9 Taonani tsiku la Yehova lidza, lankhanza, ndi mkwiyo ndi kukalipira kwaukali; kupasula dziko, ndi kudzaonongamo akuchimwa psiti.

10 Chifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m’kutuluka kwake, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.

11 Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao, ndi oipa chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsa.

12 Ndipo ndidzachepsa anthu koposa golide, ngakhale anthu koposa golide weniweni wa ku Ofiri.

13 Chifukwa chake ndidzanthunthumiritsa miyamba, ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka kuchokera m’malo ake, m’mkwiyo wa Yehova wa makamu, tsiku la mkwiyo wake waukali.

14 Ndipo padzakhala kuti monga mbawala yothamangitsidwa, ndi monga nkhosa zosazisonkhanitsa anthu, adzatembenukira yense kwa anthu ake, nathawira yense kudziko lake.

15 Onse opezedwa adzapyozedwa, ndi onse ogwidwa adzagwa ndi lupanga.

16 Makanda ao adzatswanyidwe pamaso pao; m’nyumba mwao mudzafunkhidwa, ndi akazi ao adzakakamizidwa.

17 Taonani, ndidzawautsira Amedi, amene sadzasamalirasiliva, ngakhale golide sadzakondwera naye.

18 Mauta ao adzatha anyamata; ndipo sadzachitira chisoni chipatso cha mimba; diso lao silidzaleka ana.

19 Ndipo Babiloni, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Ababiloni anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.

20 Anthu sadzakhalamo konse, sadzakhalamo mbadwo ndi mbadwo; Mwarabu sadzamanga hema wake pamenepo; abusa sadzagonetsa makamu ao kumeneko.

21 Koma zilombo za m’chipululu zidzagona pamenepo; nyumba zao zidzadzala ndi zakukuwa; ndipo nthiwatiwa zidzakhala pamenepo, ndipo atonde adzajidimuka pamenepo.

22 Ndipo mimbulu idzalira m’maboma ao, ndi ankhandwe m’manyumba ao abwino; ndi nthawi yake iyandikira, ndi masiku ake sadzachuluka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/13-a28fe9a770373adae2dcb1f0e26c0320.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *