1 Nthawi yomweyo, ati Yehova, adzatulutsa m’manda mwao mafupa a mafumu a Yuda, ndi mafupa a akulu ake, ndi mafupa a ansembe, ndi mafupa a aneneri, ndi mafupa a okhala m’Yerusalemu,
2 ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.
3 Ndipo otsala onse amene akutsala pa banja loipa ili adzasankha imfa koposa moyo, ndiwo amene atsala m’malo monse m’mene ndinawaingiramo, ati Yehova wa makamu.
Kulowerera kwa anthu a Mulungu, kulangidwa kudzafikadi
4 Ndiponso udzati kwa iwo, Atero Yehova, Kodi adzagwa, osaukanso? Kodi wina adzachoka, osabweranso?
5 Bwanji abwerera anthu awa a Yerusalemu chibwererere? Agwiritsa chinyengo, akana kubwera.
6 Ndinatchera khutu, ndinamva koma sananene bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zake, ndi kuti, Ndachita chiyani? Yense anatembenukira njira yake, monga akavalo athamangira m’nkhondo.
7 Inde, chumba cha mlengalenga chidziwa nyengo zake; ndipo njiwa ndi namzeze ndi chingalu ziyang’anira nyengo yakufika kwao; koma anthu anga sadziwa chiweruziro cha Yehova.
8 Bwanji muti, Tili ndi nzeru ife, ndi malamulo a Yehova ali ndi ife? Koma, taona, peni lonyenga la alembi lachita zonyenga.
9 Anzeru ali ndi manyazi, athedwa nzeru nagwidwa; taonani, akana mau a Yehova; ali nayo nzeru yotani?
10 Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambiramnenerikufikira wansembe onse achita zonyenga.
11 Ndipo analipoletsa pang’ono bala la mwana wamkazi wa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, mtendere; posakhala mtendere.
12 Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang’aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.
13 Kuwatha ndidzawathetsa iwo, ati Yehova, sipadzakhala mphesa pampesa, kapena nkhuyu pamkuyu, ndipo tsamba lidzafota, ndipo zinthu ndinawapatsa zidzawachokera.
14 Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m’mizinda yamalinga, tikhale chete m’menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova.
15 Tinayang’anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa!
16 Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mzinda ndi amene akhalamo.
17 Pakuti, taonani, ndidzatumiza pa inu njoka, mphiri, zosalola kuitanidwa; ndipo zidzakulumani inu, ati Yehova.
18 Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa chisoni chake? Mtima wanga walefuka m’kati mwa ine.
19 Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi muZiyonimulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo?
20 Masika apita, mphakasa yatha, ndipo ife sitinapulumutsidwe.
21 Bala la mwana wamkazi wa anthu anga ndaphwetekwa nalo; ndada mtima; kudabwa kwandigwira.
22 Kodi mulibe vunguti mu Giliyadi? Kodi mulibe sing’anga m’menemo; analekeranji kuchira mwana wamkazi wa anthu anga?
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/8-4a165454f83e51ecd48bc16941660447.mp3?version_id=1068—