Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 51

1 Yehova atero: Taonani, ndidzaukitsira Babiloni, ndi iwo okhala mu Lebi-kamai, mphepo yoononga.

2 Ndipo ndidzatuma ku Babiloni alendo, amene adzampeta iye, amene adzataya zonse m’dziko lake, pakuti tsiku la chisauko adzamenyana ndi iye pomzungulira pake.

3 Wauta asakoke uta wake, asadzikweze m’malaya ake achitsulo; musasiye anyamata ake; muononge ndithu khamu lake lonse.

4 Ndipo adzagwa ophedwa m’dziko la Ababiloni, opyozedwa m’miseu yake.

5 Pakuti Israele ndi Yuda sasiyidwa ndi Mulungu wao, ndiye Yehova wa makamu: ngakhale dziko lao ladzala ndi uchimo kuchimwira Woyera wa Israele.

6 Thawani pakati pa Babiloni, yense apulumuke moyo wake; musathedwe m’choipa chake; pakuti ndi nthawi ya kubwezera chilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yake.

7 Babiloni wakhala chikho chagolide m’dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi;amitunduamwa vinyo wake; chifukwa chake amitundu ali ndi misala.

8 Babiloni wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zake vunguti, kapena angachire.

9 Tikadachiritsa Babiloni koma sanachire; mumsiye iye, tipite tonse yense kudziko lake; pakuti chiweruziro chake chifikira kumwamba, chinyamulidwa mpaka kuthambo.

10 Yehova watulutsa chilungamo chathu; tiyeni tilalikire muZiyonintchito ya Yehova Mulungu wathu.

11 Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.

12 Muwakwezere mbendera makoma a Babiloni, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kuchita chomwe ananena za okhala mu Babiloni.

13 Iwe wokhala pamadzi ambiri, wochuluka chuma, chimaliziro chako chafika, chilekezero cha kusirira kwako.

14 Yehova wa makamu walumbira pa Iye mwini, kuti, Ndithu ndidzakudzaza iwe ndi anthu, monga ndi madzombe; ndipo adzakukwezera iwe mfuu.

15 Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, wakhazika dziko lapansi ndi nzeru yake, ndi luso anayala thambo;

16 pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m’mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, atulutsa mphepo ya m’nyumba za chuma zake.

17 Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; wakusula golide achitidwa manyazi ndi fanizo lake losema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya m’menemo.

18 Ngwachabe, chiphamaso; nthawi ya kulangidwa kwao adzatayika.

19 Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndi mtundu wa cholowa chake, dzina lake ndi Yehova wa makamu.

20 Iwe ndiwe chibonga changa ndi zida zanga za nkhondo; ndi iwe ndidzathyolathyola amitundu, ndi iwe ndidzaononga maufumu;

21 ndi iwe ndidzathyolathyola kavalo ndi wokwera wake;

22 ndi iwe ndidzathyolathyola galeta ndi iye wokweramo; ndi iwe ndidzathyolathyola mwamuna ndi mkazi; ndi iwe ndidzathyolathyola wokalamba ndi mnyamata; ndi iwe ndidzathyolathyola mnyamata ndi namwali;

23 ndi iwe ndidzathyolathyola mbusa ndi zoweta zake; ndi iwe ndidzathyolathyola wakulima ndi goli la ng’ombe lake; ndi iwe ndidzathyolathyola akazembe ndi ziwanga.

24 Ndipo ndidzabwezera Babiloni ndi okhala mu Kasidi zoipa zao zonse anazichita mu Ziyoni pamaso panu, ati Yehova.

25 Taona, ndimenyana ndi iwe, iwe phiri lakuononga, ati Yehova, limene liononga dziko lonse; ndipo ndidzakutambasulira iwe dzanja langa, ndipo ndidzakugubuduza iwe kumatanthwe, ndipo ndidzakuyesa iwe phiri lotenthedwa.

26 Ndipo sadzachotsa pa iwe mwala wa pangodya, kapena mwala wa pamaziko; koma udzakhala bwinja nthawi zonse, ati Yehova.

27 Kwezani mbendera m’dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenazi; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati dzombe.

28 Konzerani amitundu amenyane ndi iye, mafumu a Amedi, akazembe ake, ndi ziwanga zake zonse, ndi dziko lonse la ufumu wake.

29 Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babiloni zilipobe, zoti ayese dziko la Babiloni bwinja lopanda wokhalamo.

30 Olimba a ku Babiloni akana kumenyana, akhala m’malinga ao; mphamvu yao yalephera; akhala ngati akazi; nyumba zake zapsa ndi moto; akapichi ake athyoka.

31 Wamtokoma mmodzi adzathamanga kukakomana ndi mnzake, ndi mthenga mmodzi kukomana ndi mnzake, kukauza mfumu ya ku Babiloni kuti mzinda wake wagwidwa ponsepo;

32 pamadooko patsekedwa, pamatamanda a mabango patenthedwa ndi moto, ndi anthu a nkhondo aopa.

33 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwana wamkazi wa Babiloni akunga dwale pamene aliunda; patsala kanthawi kakang’ono, ndipo nthawi yamasika idzamfikira iye.

34 Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng’ona, wadzaza m’kamwa mwake ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine.

35 Wokhala mu Ziyoni adzati, Chiwawa anandichitira ine ndi thupi langa chikhale pa Babiloni; nadzatiYerusalemu, Mwazi wanga ukhale pa okhala mu Kasidi.

36 Chifukwa chake Yehova atero: Taona, ndidzanenera iwe mlandu wako, ndidzawabwezera chilango chifukwa cha iwe; ndidzaphwetsa nyanja yake, ndidzaphwetsa chitsime chake.

37 Ndipo Babiloni adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, chizizwitso, chotsonyetsa, wopanda okhalamo.

38 Adzabangula pamodzi ngati misona ya mikango; adzachita nthulu ngati ana a mikango.

39 Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone chigonere, asanyamuke, ati Yehova.

40 Ndidzawagwetsa kuti aphedwe monga anaankhosa amphongo, ndi atonde.

41 Sesaki wagwidwatu! Chimene dziko lonse lapansi linachitamanda chalandidwa dzidzidzi! Babiloni wakhalatu bwinja pakati pa amitundu!

42 Nyanja yakwera kufikira ku Babiloni; wamira ndi mafunde ake aunyinji.

43 Mizinda yake yakhala bwinja, dziko louma, chipululu mosakhalamo anthu, mosapita mwana wa munthu aliyense.

44 Ndipo Ine ndiweruza Beli mu Babiloni, ndipo ndidzatulutsa m’kamwa mwake chomwe wachimeza; ndipo amitundu sadzasonkhaniranso konse kwa iye; inde, khoma la Babiloni lidzagwa.

45 Anthu anga, tulukani pakati pake, mudzipulumutse munthu yense ku mkwiyo waukali wa Yehova.

46 Mtima wanu usalefuke, musaope chifukwa cha mbiri imene idzamveka m’dzikomu; pakuti mbiri idzafika chaka china, pambuyo pake chaka china mbiri ina, ndi chiwawa m’dziko, wolamulira kumenyana ndi wolamulira.

47 Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babiloni, ndipo dziko lake lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ake onse adzagwa pakati pake.

48 Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zonse zili m’menemo, zidzaimba mokondwerera Babiloni; pakuti akufunkha adzafika kwa iye kuchokera kumpoto, ati Yehova.

49 Monga Babiloni wagwetsa ophedwa a Israele, momwemo pa Babiloni padzagwa ophedwa a dziko lonse.

50 Inu amene mwapulumuka kulupanga, pitani inu musaime chiimire; mukumbukire Yehova kutali, Yerusalemu alowe m’mtima mwanu.

51 Tili ndi manyazi, chifukwa tamva mnyozo; manyazi aphimba nkhope zathu; pakuti alendo alowa m’malo opatulika a nyumba ya Yehova.

52 Chifukwa chake, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ake; ndipo padziko lake lonse olasidwa adzabuula.

53 Ngakhale Babiloni adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yake, koma kuchokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova.

54 Mau akufuula ochokera ku Babiloni, ndi a chionongeko chachikulu ku dziko la Ababiloni!

55 Pakuti Yehova afunkha Babiloni, aononga m’menemo mau aakulu; ndipo mafunde ake adzakokoma ngati madzi ambiri, mau ao apokosera;

56 pakuti wakufunkha wafika kwa iye, kwa Babiloni, ndi anthu ake olimba agwidwa, mauta ao athyokathyoka, pakuti Yehova ndiye Mulungu wakubwezera, adzabwezera ndithu.

57 Ndipo ndidzaledzeretsa akulu ake ndi anzeru ake, akazembe ake ndi ziwanga zake, ndi anthu ake olimba; ndipo adzagona chigonere, sadzanyamuka, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu.

58 Yehova wa makamu atero: Makoma otakata a Babiloni adzagwetsedwa ndithu, ndi zitseko zake zazitali zidzatenthedwa ndi moto; anthu adzagwirira ntchito chabe, ndi mitundu ya anthu idzagwirira moto, nidzatopa.

59 Mau amene Yeremiyamnenerianauza Seraya mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamene iye ananka ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babiloni chaka chachinai cha ufumu wake. Ndipo Seraya anali kapitao wa chigono chake.

60 Ndipo Yeremiya analemba m’buku choipa chonse chimene chidzafika pa Babiloni, mau onse awa olembedwa za Babiloni.

61 Ndipo Yeremiya anati kwa Seraya, Pamene ufika ku Babiloni, samalira kuti uwerenge mau awa onse,

62 nuti, Inu Yehova, mwanena za malo ano, kuti mudzawatha, kuti asakhalemo, ngakhale anthu ngakhale nyama, koma akhale bwinja nthawi za nthawi.

63 Ndipo padzakhala, utatha kuwerenga buku ili, ulimange ndi mwala, nuliponye pakati pa Yufurate;

64 nuti, Chomwecho adzamira Babiloni, sadzaukanso chifukwa cha choipa chimene ndidzamtengera iye; ndipo adzatopa. Mau a Yeremiya ndi omwewo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/51-11ede718d16c300df5b8bb1781d98078.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *