Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 49

Chitsutso cha Aamoni

1 Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israele alibe ana aamuna? Alibe wolowa dzina? M’mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi chifukwa chanji, ndi anthu ake akhala m’mizinda mwake?

2 Chifukwa chake, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo midzi yake idzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israele adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova.

3 Kuwa, iwe Hesiboni, pakuti Ai wapasuka; lirani, inu ana aakazi a Raba, muvale chiguduli; chitani maliro, thamangani kwina ndi kwina pamipanda; pakuti mfumu yao idzalowa m’ndende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.

4 Chifukwa chanji udzitamandira ndi zigwa, chigwa chako choyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m’mbuyo, amene anakhulupirira chuma chake, nati, Adza kwa ine ndani?

5 Taona ndidzakutengera mantha, ati Ambuye, Yehova wa makamu, akuchokera kwa onse amene akuzungulira iwe; ndipo mudzaingitsidwa yense kulozera maso ake, ndipo palibe amene adzasonkhanitsa osochera.

6 Koma pambuyo pake ndidzabwezanso undende wa ana a Amoni, ati Yehova.

Za kulangidwa kwa Aedomu

7 Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi mu Temani mulibenso nzeru? Kodi uphungu wawathera akuchenjera? Kodi nseru zao zatha psiti?

8 Thawani inu, bwerani, khalani mwakuya, inu okhala mu Dedani; pakuti ndidzatengera pa iye tsoka la Esau, nthawi yoti ndidzamlanga iye.

9 Akafika kwa inu akutchera mphesa, sadzasiya mphesa zokunkha? Akafika usiku akuba, adzaononga mpaka kutha?

10 Pakuti ndamvula Esau, ndamvundukula, sadzatha kubisala; mbeu zake zaonongeka, ndi abale ake, ndi anansi ake, ndipo palibe iye.

11 Siya ana ako amasiye, Ine ndidzawasunga; akazi ako amasiye andikhulupirire Ine.

12 Pakuti Yehova atero: Taonani, iwo amene sanaweruzidwe kuti amwe chikho adzamwadi; kodi iwe ndiye amene adzakhala wosalangidwa konse? Sudzakhala wosalangidwa, koma udzamwadi.

13 Pakuti ndalumbira, Pali Ine ati Yehova, kuti Bozira adzakhala chizizwitso, chitonzo, chopasuka, ndi chitemberero; ndipo mizinda yake yonse idzakhala yopasuka chipasukire.

14 Ndamva mthenga wa kwa Yehova, ndipo mthenga watumidwa mwaamitundu, wakuti, Sonkhanani, mumdzere, nimuukire nkhondo.

15 Pakuti, taona, ndakuyesa iwe wamng’ono mwa amitundu, ndi wonyozedwa mwa anthu.

16 Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m’mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.

17 Ndipo Edomu adzakhala chizizwitso; ndipo yense wakupitapo adzazizwa, ndipo adzatsonyera zovuta zake zonse.

18 Monga m’kupasuka kwa Sodomu ndi Gomora ndi mizinda inzake, ati Yehova, munthu aliyense sadzakhala m’menemo, mwana wa munthu aliyense sadzagona m’menemo.

19 Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amchokere; ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang’anira wake, pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?

20 Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala mu Temani, ndithu adzawakoka, ana aang’ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.

21 Dziko lapansi linthunthumira ndi phokoso la kugwa kwao; pali mfuu, phokoso lake limveka pa Nyanja Yofiira.

22 Taonani, adzafika nadzauluka ngati chiombankhanga, adzatambasulira Bozira mapiko ake, ndipo tsiku lomwemo mtima wa anthu amphamvu a Edomu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.

Chitsutso cha Damasiko

23 Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, chifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala chete.

24 Damasiko walefuka, atembenukira kuti athawe, kunthunthumira kwamgwira; zovuta ndi kulira zamgwira iye, ngati mkazi alimkudwala.

25 Alekeranji kusiya mzinda wa chilemekezo, mzinda wa chikondwero changa?

26 Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m’miseu yake, ndipo anthu onse a nkhondo adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu.

27 Ndipo Ine ndidzayatsa moto m’khoma la Damasiko, udzathetsa zinyumba za Benihadadi.

Chitsutso cha Kedara ndi Hazori

28 Za Kedara, ndi za maufumu a Hazori, amene anawakantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Yehova atero: Ukani, kwerani ku Kedara, funkhani ana a ku m’mawa.

29 Mahema ao ndi zoweta zao adzazilanda, adzadzitengera nsalu zotchingira zao, ndi katundu wao yense, ndingamirazao; ndipo adzafuulira iwo, Mantha ponseponse.

30 Thawani inu, yendani kutali, khalani mwakuya, Inu okhala mu Hazori, ati Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anapangira uphungu pa inu, nakulingalirirani.

31 Nyamukani, kwererani mtundu wokhala ndi mtendere, wokhala osadera nkhawa, ati Yehova, amene alibe zitseko ndi mapiringidzo, okhala pa okha.

32 Ndipo ngamira zao zidzakhala zofunkha, ndi unyinji wa ng’ombe zao udzakhala wolanda; ndipo ndidzabalalitsira kumphepo zonse iwo amene ameta m’mbali mwa tsitsi lao; ndipo ndidzatenga tsoka lao kumbali zao zonse, ati Yehova.

33 Ndipo Hazori adzakhala mokhalamo ankhandwe, bwinja lachikhalire; simudzakhalamo munthu, simudzagonamo mwana wa munthu.

Chitsutso cha Elamu

34 Mau a Yehova amene anafika kwa Yeremiyamneneri, onena za Elamu poyamba kulamulira Zedekiya mfumu ya Yuda, kuti,

35 Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu, ndiwo mtima wa mphamvu yao.

36 Pa Elamu ndidzatengera mphepo zinai kumbali zinai za mlengalenga, ndidzamwaza iwo kumphepo zonsezo; ndipo sikudzakhala mtundu kumene opirikitsidwa a Elamu sadzafikako.

37 Ndipo ndidzachititsa Elamu mantha pamaso pa amaliwongo ao, ndi pamaso pa iwo ofuna moyo wao; ndipo ndidzatengera choipa pa iwo, mkwiyo wanga waukali, ati Yehova; ndipo ndidzatumiza lupanga liwalondole, mpaka nditawatha;

38 ndipo ndidzaika mpando wachifumu wanga mu Elamu, ndipo ndidzaononga pamenepo mfumu ndi akulu, ati Yehova.

39 Koma padzaoneka masiku akutsiriza, kuti ndidzabwezanso undende wa Elamu, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/49-47c3d8ad9be05146370e0b170fc41d10.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *