Aneneratu kuti mfumu ya ku Babiloni idzagonjetsa Aejipito
1 Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiyamneneriakunena zaamitundu.
2 Za Ejipito: kunena za nkhondo yaFaraoNeko mfumu ya Aejipito, imene inali pamtsinje wa Yufurate mu Karikemisi, imene anaikantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda.
3 Konzani chikopa ndi lihawo, nimuyandikire kunkhondo.
4 Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zazitsulo; tuulani nthungo zanu, valani malaya achitsulo.
5 Chifukwa chanji ndachiona? Aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osacheukira m’mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.
6 Waliwiro asathawe, wamphamvu asapulumuke; kumpoto pambali pamtsinje wa Yufurate waphunthwa nagwa.
7 Ndani uyu amene auka ngati mtsinje, madzi ake ogavira monga mitsinje?
8 Ejipito auka ngati mtsinje, madzi ake agavira ngati mitsinje; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mizinda ndi okhalamo ake.
9 Kwerani, inu akavalo; chitani misala, inu magaleta, atuluke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira chikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.
10 Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza chilango, kuti abwezere chilango adani ake; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m’dziko la kumpoto pamtsinje wa Yufurate.
11 Kwera ku Giliyadi, tenga vunguti, namwali iwe mwana wa Ejipito; wachulukitsa mankhwala chabe; palibe kuchira kwako.
12 Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kufuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi.
13 Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adzafika adzakantha dziko la Ejipito.
14 Nenani mu Ejipito, lalikirani mu Migidoli, lalikirani mu Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.
15 Akulimba ako akokoledwa bwanji? Sanaime, chifukwa Yehova anawathamangitsa.
16 Anaphunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzake, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, kudziko la kubadwa kwathu, kuchokera kulupanga lovutitsa.
17 Ndipo anafuula kumeneko, Farao mfumu ya Aejipito ndiye phokoso lokha; wapititsa nthawi yopangira.
18 Pali Ine, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimele pambali pa nyanja, momwemo adzafika.
19 Mwana wamkazi iwe wokhala mu Ejipito, dzikonzere kunka kundende; pakuti Nofi adzakhala bwinja, nadzapsa, mulibenso wokhalamo.
20 Ejipito ndi ng’ombe yaikazi yosalala; chionongeko chotuluka kumpoto chafika, chafika.
21 Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang’ombe a m’khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.
22 Mkokomo wake udzanga wa njoka yothawa; pakuti adzayenda ndi nkhondo, adzafika kumenyana naye ndi nkhwangwa, monga akutema mitengo.
23 Adzatema nkhalango yake, ati Yehova, pokhala yosapitika; pakuti achuluka koposa dzombe, ali osawerengeka.
24 Mwana wake wamkazi wa Ejipito adzachitidwa manyazi, adzaperekedwa m’manja a anthu a kumpoto.
25 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, ati, Taonani, ndidzalanga Amoni wa No, ndi Farao, ndi Ejipito, pamodzi ndi milungu yake, ndi mafumu ake; ngakhale Farao, ndi iwo akumkhulupirira iye;
26 ndipo ndidzawapereka m’manja a iwo amene afuna moyo wao, ndi m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m’manja a atumiki ake; pambuyo pake adzakhalamo anthu, monga masiku akale, ati Yehova.
27 Koma usaope iwe, mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha, iwe Israele: pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kuchokera kutali, ndi mbeu yako kudziko la undende wao, ndipo Yakobo adzabwera, nadzapumula m’mtendere, ndipo palibe amene adzamuopetsa iye.
28 Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndili ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi chiweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/46-d06c551d0b144f7a2231002a4b099d55.mp3?version_id=1068—