Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 41

Gedaliya ndi ena aphedwa ndi Ismaele

1 Ndipo panali mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaele mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa mbeu ya mfumu, ndi kapitao wamkulu wa mfumu, ndi anthu khumi pamodzi ndi iye, anadza kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa; pamenepo anadya pamodzi mu Mizipa.

2 Ndipo anauka Ismaele mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babiloni inamuika wolamulira dziko.

3 Ismaele naphanso Ayuda onse okhala naye Gedaliya pa Mizipa, ndi Ababiloni amene anakomana nao komweko, amuna a nkhondo.

4 Ndipo panali atapita masiku awiri atamupha Gedaliya, anthu osadziwa,

5 anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang’amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndilubanim’manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova.

6 Ndipo Ismaele mwana wa Netaniya anatuluka mu Mizipa kukakomana nao, alinkuyenda ndi kulira misozi; ndipo panali, pamene anakomana nao, anati kwa iwo, Idzani kwa Gedaliya mwana wake wa Ahikamu.

7 Ndipo panali, pamene analowa pakati pa mzinda, Ismaele mwana wa Netaniya anawapha, nawaponya pakati pa dzenje, iye ndi anthu okhala naye.

8 Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismaele, Musatiphe ife; pakuti tili ndi chuma chobisika m’mudzi, cha tirigu, ndi cha barele, ndi cha mafuta, ndi cha uchi. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao.

9 Ndipo dzenje moponyamo Ismaele mitembo yonse ya anthu amene anawapha, chifukwa cha Gedaliya, ndilo analipanga mfumu Asa chifukwa cha kuopa Baasa mfumu ya Israele, lomwelo Ismaele mwana wa Netaniya analidzaza ndi ophedwawo.

10 Ndipo Ismaele anatenga ndende otsala onse a anthu okhala mu Mizipa, ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene anatsala mu Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismaele mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni.

11 Koma pamene Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo akhala naye, anamva zoipa zonse anazichita Ismaele mwana wa Netaniya,

12 anatenga anthu onse, nanka kukamenyena ndi Ismaele mwana wa Netaniya, nampeza pamadzi ambiri a mu Gibiyoni.

13 Ndipo panali pamene anthu onse amene anali ndi Ismaele anaona Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, anasekera.

14 Ndipo anthu onse amene Ismaele anatenga ndende kuwachotsa mu Mizipa anatembenuka nabwera, nanka kwa Yohanani mwana wake wa Kareya.

15 Koma Ismaele mwana wake wa Netaniya anapulumuka Yohanani ndi anthu asanu ndi atatu, nanka kwa ana a Amoni.

16 Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya ndi akazembe onse a makamu amene anali naye, anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa, amene anawabweza kwa Ismaele mwana wake wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, anthu a nkhondo, ndi akazi, ndi ana, ndi adindo, amene anawabwezanso ku Gibiyoni;

17 ndipo anachoka, natsotsa mu Geruti-Kimuhamu, amene ali ku Betelehemu, kunka kulowa mu Ejipito,

18 chifukwa cha Ababiloni; pakuti anawaopa, chifukwa Ismaele mwana wake wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babiloni anamuika wolamulira m’dzikomo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/41-b9aaab098fe54b2eec566100a7bba58e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *