1 Ngati udzabwera, Israele, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzachotsa zonyansa zako pamaso panga sudzachotsedwa.
2 Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m’zoonadi, m’chiweruziro, ndi m’chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.
Adani achilendo adzagwera dziko la Yuda
3 Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwaYerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga.
4 Mudzidulire nokha kwa Yehova, chotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala mu Yerusalemu; ukali wanga ungatuluke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe anu.
5 Nenani mu Yuda, lalikirani mu Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m’dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m’mizinda ya malinga.
6 Kwezani mbendera kuyang’ana kuZiyoni; thawani kuti mupulumuke, musakhale; pakuti ndidza ndi choipa chochokera kumpoto ndi kuononga kwakukulu.
7 Mkango wakwera kutuluka m’nkhalango mwake, ndipo waononga amitundu ali panjira, watuluka m’mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti mizinda yako ipasuke mulibenso wokhalamo.
8 Pamenepo, valani chiguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wa kuopsa wa Yehova sunabwerere pa ife.
9 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, kuti mtima wa mfumu udzataika, ndi mitima ya akulu; ndipo ansembe adzazizwa, ndi aneneri adzadabwa.
10 Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! Ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.
11 Pa nthawi yomweyo adzati kwa anthu awa ndi kwa Yerusalemu, Mphepo yotentha yochokera kumapiri oti see m’chipululu yopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga, yosapetera, yosayeretsa;
12 mphepo yolimba yochokera kumeneko idzandifika ine; tsopanonso ndidzaweruza iwo maweruzo.
13 Taonani, adzadza ngati mitambo, ndi magaleta ake ngati kamvulumvulu; akavalo ake athamanga kopambana mphungu. Tsoka ife! Pakuti tapasuka.
14 Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?
15 Pakuti mau anena mu Dani nalalikira nsautso m’phiri la Efuremu:
16 Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira kudziko lakutali, nainenera mizinda ya Yuda mau ao.
17 Monga adindo a m’munda amzinga iye; chifukwa andipandukira Ine, ati Yehova.
18 Njira yako ndi ntchito zako zinakuchitira izi; ichi ndicho choipa chako ndithu; chili chowawa ndithu, chifikira kumtima wako.
19 Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m’kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.
20 Alalikira chipasuko chilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsalu zanga zotchinga m’kamphindi.
21 Kufikira liti ndidzaona mbendera, ndi kumva kulira kwa lipenga?
22 Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.
23 Ndinaona dziko lapansi, ndipo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika.
24 Ndinaona mapiri, taona ananthunthumira; ndipo zitunda zonse zinagwedezeka.
25 Ndinaona, ndipo taona, panalibe munthu, ndi mbalame zonse zakumwamba zinathawa.
26 Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali chipululu, ndipo mizinda yake yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wake woopsa.
27 Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa.
28 Chifukwa chimenecho dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; chifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo.
29 Mzinda wonse uthawa m’phokoso la apakavalo ndi amauta; adzalowa m’nkhalango, adzakwera pamiyala; mizinda yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu m’menemo.
30 Nanga iwe, udzachita chiyani pamene udzafunkhidwa? Ngakhale udziveka ndi zofiira, ngakhale udziveka ndi zokometsera zagolide, ngakhale udzikuzira maso ako ndi kupaka, udzikometsera pachabe; mabwenzi adzakunyoza adzafuna moyo wako.
31 Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/4-5551d613fb2f1bba364043c0d98fb43c.mp3?version_id=1068—