Yeremiya m’kaidi
1 Ndipo Zedekiya mwana wa Yosiya anakhala mfumu m’malo a Koniya mwana wa Yehoyakimu, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni inamlowetsa mfumu m’dziko la Yuda.
2 Koma ngakhale iye, ngakhale atumiki ake, ngakhale anthu a padziko, sanamvere mau a Yehova, amene ananena mwa Yeremiya mneneri.
3 Ndipo Zedekiya mfumu anatuma Yehukala mwana wa Selemiya, ndi Zefaniya mwana wa Maaseiya wansembe, kwa Yeremiya mneneri, kukanena, Mutipemphereretu kwa Yehova Mulungu wathu.
4 Ndipo Yeremiya analikuyendayenda mwa anthu; chifukwa sanamuike iye m’nyumba yandende.
5 Ndipo nkhondo yaFaraoinatuluka mu Ejipito; ndipo pamene Ababiloni omangira misasaYerusalemuanamva mbiri yao, anachoka ku Yerusalemu.
6 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya mneneri, kuti,
7 Atero Yehova, Mulungu wa Israele: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakutulukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Ejipito ku dziko lao.
8 Ndipo Ababiloni adzabweranso, nadzamenyana ndi mzinda uwu; ndipo adzaulanda, nadzautentha ndi moto.
9 Yehova atero: Musadzinyenge, kuti, Ababiloni adzatichokera ndithu; pakuti sadzachoka.
10 Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Ababiloni akumenyana nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okhaokha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m’hema wake ndi kutentha mzinda uwu ndi moto.
11 Ndipo panali pamene nkhondo ya Ababiloni inachoka ku Yerusalemu chifukwa cha nkhondo ya Farao,
12 pamenepo Yeremiya anatuluka mu Yerusalemu kumuka kudziko la Benjamini, kukalandira gawo lake kumeneko.
13 Pokhala iye mu Chipata cha Benjamini, kapitao wa alonda anali kumeneko, dzina lake Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya; ndipo iye anamgwira Yeremiya mneneri, nati, Ulinkupandukira kwa Ababiloni.
14 Ndipo anati Yeremiya, Kunama kumeneko; ine sindipandukira kwa Ababiloni; koma sanamvere iye; ndipo Iriya anamgwira Yeremiya, nanka naye kwa akulu.
15 Ndipo akulu anakwiyira Yeremiya, nampanda iye, namuika m’nyumba yandende m’nyumba ya Yonatani mlembi; pakuti anaiyesa ndende.
16 Atafika Yeremiya kunyumba yadzenje, ku tizipinda take nakhalako Yeremiya masiku ambiri;
17 pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m’tseri m’nyumba mwake, niti, Kodi alipo mau ochokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo. Anatinso, Mudzaperekedwa m’dzanja la mfumu ya ku Babiloni.
18 Ndipo Yeremiya anati kwa mfumu Zedekiya, Ndachimwira inu chiyani, kapena atumiki anu, kapena anthu awa, kuti mwandiika m’nyumba yandende?
19 Tsopano ali kuti aneneri anu, amene ananenera inu, kuti, Mfumu ya ku Babiloni sidzakudzerani inu, kapena dziko lino?
20 Tsopano tamvanitu, mbuyanga mfumu; pembedzero langa ligwe pamaso panu; kuti musandibwezere kunyumba ya Yonatani mlembi, ndingafe kumeneko.
21 Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m’bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma kumseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m’mzinda. Ndipo Yeremiya anakhala m’bwalo la kaidi.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/37-731da6219102e7766b994b7aceb04e4f.mp3?version_id=1068—