Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 36

Mau a Yeremiya alembedwa pampukutu nawerengedwa mu Kachisi, natenthedwa ndi mfumu

1 Ndipo panali chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,

2 Tenga buku lampukutu, nulembe m’menemo mau onse ndanena kwa iwe akunenera Israele, ndi akunenera Yuda, ndi akuneneraamitunduonse kuyambira tsiku ndinanena kwa iwe, kuyambira masiku a Yosiya, mpaka lero.

3 Kapena nyumba ya Yuda idzamva choipa chonse chimene nditi ndidzawachitire; kuti abwerere yense kuleka njira yake yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi tchimo lao.

4 Ndipo Yeremiya anaitana Baruki mwana wa Neriya; ndipo Yeremiya analembetsa Baruki m’buku lampukutu mau onse a Yehova, amene ananena naye.

5 Ndipo Yeremiya anauza Baruki, kuti, Ndaletsedwa sindithai kulowa m’nyumba ya Yehova;

6 koma pita iwe, nuwerenge mu mpukutu umene ndakulembetsa, mau a Yehova m’makutu a anthu m’nyumba ya Yehova tsiku lakusala kudya; ndiponso udzawawerenga m’makutu a Ayuda onse amene atuluka m’mizinda yao.

7 Kapena pembedzero lao lidzagwa pamaso pa Yehova, ndipo adzabwerera yense kuleka njira yake yoipa; pakuti mkwiyo ndi ukali umene Yehova wanenera anthu awa ndi waukulu.

8 Ndipo Baruki mwana wa Neriya anachita monga mwa zonse anamuuza iye Yeremiyamneneri, nawerenga m’buku mau a Yehova m’nyumba ya Yehova.

9 Ndipo panali chaka chachisanu cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mwezi wachisanu ndi chinai, anthu onse a muYerusalemu, ndi anthu onse ochokera m’mizinda ya Yuda kudza ku Yerusalemu, analalikirakusala kudyapamaso pa Yehova.

10 Ndipo Baruki anawerenga m’buku mau a Yeremiya m’nyumba ya Yehova, m’chipinda cha Gemariya mwana wa Safani mlembi, m’bwalo la kumtunda, pa khomo la Chipata Chatsopano cha nyumba ya Yehova, m’makutu a anthu onse.

11 Pamene Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani, anamva m’buku mau onse a Yehova,

12 anatsikira kunyumba ya mfumu, nalowa m’chipinda cha mlembi; ndipo, taonani, akulu onse analikukhalamo, Elisama mlembi, ndi Delaya mwana wa Semaya, ndi Elinatani mwana wa Akibori, ndi Gemariya mwana wa Safani, ndi Zedekiya mwana wa Hananiya, ndi akulu onse.

13 Ndipo Mikaya anafotokozera iwo mau onse amene anamva, pamene Baruki anawerenga buku m’makutu a anthu.

14 Chifukwa chake akulu onse anatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki, kukanena, Tenga m’dzanja lako mpukutu wauwerenga m’makutu a anthu, nudze kuno. Ndipo Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo m’dzanja lake, nadza kwa iwo.

15 Ndipo anati kwa iye, Khala pansi tsopano, nuwerenga m’makutu athu. Ndipo Baruki anauwerenga m’makutu ao.

16 Ndipo panali, pamene anamva mau onse, anaopa nayang’anana wina ndi mnzake, nati kwa Baruki, Tidzamfotokozeratu mfumu mau awa onse.

17 Ndipo anamfunsa Baruki, kuti, Utifotokozeretu, Unalemba bwanji mau awa onse ponena iye?

18 Ndipo Baruki anayankha iwo, Pakamwa pake ananditchulira ine mau awa onse, ndipo ndinawalemba ndi inki m’bukumo.

19 Ndipo akulu anati kwa Baruki, Pita, nubisale iwe ndi Yeremiya; munthu yense asadziwe kumene muli.

20 Ndipo analowa kwa mfumu kubwalo; ndipo anasunga buku m’chipinda cha Elisama mlembi; nafotokozera mau onse m’makutu a mfumu.

21 Ndipo mfumu anatuma Yehudi atenge mpukutuwo; ndipo anautenga kutuluka nao m’chipinda cha Elisama mlembi. Ndipo Yehudi anauwerenga m’makutu a mfumu, ndi m’makutu a akulu onse amene anaima pambali pa mfumu.

22 Ndipo mfumu anakhala m’nyumba ya nyengo yachisanu mwezi wachisanu ndi chinai; ndipo munali moto m’mbaula pamaso pake.

23 Ndipo panali, pamene Yehudi anawerenga masamba atatu pena anai, mfumu inawadula ndi kampeni ka mlembi, niwaponya m’moto wa m’mbaulamo, mpaka mpukutu wonse unatha kupsa ndi moto wa m’mbaulamo.

24 Ndipo sanaope, sanang’ambe nsalu zao, kapena mfumu, kapena atumiki ake aliyense amene anamva mau onsewa.

25 Tsononso Elinatani ndi Delaya ndi Gemariya anapembedzera mfumu kuti asatenthe mpukutuwo; koma anakana kumvera.

26 Ndipo mfumu inauza Yerameele mwana wake wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Aziriele, ndi Selemiya mwana wa Abideele, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.

27 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, mfumu itatentha mpukutuwo, ndi mau amene analemba Baruki ponena Yeremiya, kuti,

28 Tenganso mpukutu wina, nulembe m’menemo mau oyamba aja anali mu mpukutu woyamba uja, umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda wautentha.

29 Ndipo za Yehoyakimu mfumu ya Yuda uziti, Yehova atero: Iwe watentha mpukutu uwu, ndi kuti, Bwanji walemba m’menemo, kuti, Mfumu ya ku Babiloni idzadzadi nidzaononga dziko ili, nidzatha m’menemo anthu ndi nyama?

30 Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wachifumu wa Davide; ndipo mtembo wake udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli chisanu.

31 Ndipo ndidzamlanga iye ndi mbeu zake ndi atumiki ake chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzawatengera iwo, ndi okhala mu Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, zoipa zonse ndawanenera iwo, koma sanamvere.

32 Ndipo Yeremiya anatenga mpukutu wina, naupereka kwa Baruki mlembi, mwana wa Neriya; amene analemba m’menemo ponena Yeremiya mau onse a m’buku lija Yehoyakimu mfumu ya Yuda analitentha m’moto; ndipo anaonjezapo mau ambiri oterewa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/36-3fca11dc016c7b095ae97734cdf1cc5e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *