Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 33

Yehova abwereza kunena kuti anthu ake adzakhazikikanso m’dziko mwao, padzakhalanso mphukira

1 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya nthawi yachiwiri, pamene iye anali chitsekedwere m’bwalo la kaidi, kuti,

2 Atero Yehova wochita zake, Yehova wolenga zake kuti azikhazikitse; dzina lake ndi Yehova:

3 Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe, ndipo ndidzakusonyeza iwe zazikulu, ndi zopambana, zimene suzidziwa.

4 Pakuti atero Yehova, Mulungu wa Israele, za nyumba za mzinda uno, ndi za nyumba za mafumu a Yuda’zi, zinagwetsedwa ziwatchinjirizire mitumbira, ndi lupanga:

5 Adza kumenyana ndi Ababiloni, koma adzangozidzaza ndi mitembo ya anthu, amene ndawapha m’mkwiyo wanga ndi mu ukali wanga, amene ndabisira mzinda uno nkhope yanga chifukwa cha zoipa zao zonse.

6 Taonani, ndidzautengera moyo ndi kuuchiritsa, ndi kuwachiritsa; ndipo ndidzawaululira iwo kuchuluka kwa mtendere ndi zoona.

7 Ndipo ndidzabweza undende wa Yuda ndi wa Israele, ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, monga poyamba paja.

8 Ndipo ndidzawayeretsa kuchotsa mphulupulu yao, imene anandichimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandichimwira, nandilakwira Ine.

9 Ndipo ndidzayesa mzinda uno chifukwa cha kukondwa, ndi chiyamiko ndi ulemerero, pamaso paamitunduonse a padziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawachitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira chifukwa cha zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzauchitira.

10 Atero Yehova: M’malo muno, m’mene muti, Ndi bwinja, mopanda munthu, mopanda nyama, m’mizinda ya Yuda, m’makwalala aYerusalemu, amene ali bwinja, opanda munthu, opanda wokhalamo, opanda nyama,

11 mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m’nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.

12 Yehova wa makamu atero: M’malo muno, muli bwinja, mopanda munthu ndi nyama, m’mizinda yake yonse, mudzakhalanso mokhalamo abusa ogonetsa zoweta zao.

13 M’mizinda ya kumtunda, m’mizinda ya kuchidikha, m’mizinda ya kumwera, m’dziko la Benjamini, m’malo ozungulira Yerusalemu, m’mizinda ya Yuda, zoweta zidzapitanso pansi pa manja a iye amene aziwerenga, ati Yehova.

14 Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzakhazikitsa mau abwino aja ndinanena za nyumba ya Israele ndi za nyumba ya Yuda.

15 Masiku aja, nthawi ija, ndidzamphukutsira Davide mphukira ya chilungamo; ndipo adzachita chiweruzo ndi chilungamo m’dzikomu.

16 Masiku omwewo Yuda adzapulumutsidwa, ndi Yerusalemu adzakhala mokhulupirika; ili ndi dzina adzatchedwa nalo, Yehova ndiye chilungamo chathu.

17 Pakuti Yehova atero: Davide sadzasowa munthu wokhala pa mpando wachifumu wa nyumba ya Israele;

18 ndiponso ansembe a fuko la Levi sadzasowa munthu pamaso panga wakupereka nsembe zopsereza, ndi kutentha nsembe zaufa, ndi wakuchita nsembe masiku onse.

19 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,

20 Pakuti Yehova atero: Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku, m’nyengo yao;

21 pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wake; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.

22 Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mchenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; chomwecho ndidzachulukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.

23 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,

24 Kodi sulingalira chomwe anena anthu awa, kuti, Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, wataya iwo? Chomwecho anyoza anthu anga, kuti asakhalenso mtundu pamaso pao.

25 Yehova atero: Likaleka kukhala pangano langa la usana ndi usiku, ngati sindinalemba malemba a kumwamba ndi dziko lapansi;

26 pamenepo ndidzatayanso mbeu ya Yakobo, ndi ya Davide mtumiki wanga, kuti sindidzatenganso za mbeu zake kuti zikhale zolamulira mbeu za Abrahamu, ndi za Isaki, ndi za Yakobo; pakuti ndidzabweza undende wao, ndipo ndidzawachitira chifundo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/33-a575237a23ca2d5aaafb9b5b2cae67be.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *