Categories
YEREMIYA

YEREMIYA 30

Yehova alonjeza kubweza undende wa anthu a Israele

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,

2 Atero Yehova, Mulungu wa Israele, kuti, Lemba m’buku mau onse amene ndanena kwa iwe.

3 Pakuti, taona, masiku adzadza, ati Yehova, amene ndidzabwezanso undende wa anthu anga Aisraele ndi Ayuda, ati Yehova; ndipo ndidzawabwezera kudziko limene ndinapatsa makolo ao. Ndipo adzakhala nalo.

4 Awa ndi mau ananena Yehova za Israele ndi Yuda.

5 Pakuti Yehova atero: Tamva ife mau akunthunthumira, ndi amantha, si amtendere.

6 Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; chifukwa chanji ndiona mwamuna ndi manja ake pa chuuno chake, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka?

7 Kalanga ine! Pakuti nlalikulu tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m’menemo.

8 Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzathyola goli lake pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;

9 koma adzamtumikira Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, imene Ndidzawaukitsira.

10 Ndipo usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; usaope, iwe Israele; pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kutali, ndi mbeu zako kudziko la undende wao; ndipo Yakobo adzabwera, nadzakhala ndi mtendere, ndipo adzakhala chete, palibe amene adzamuopsa.

11 Pakuti Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi chiweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosapalamula.

12 Pakuti atero Yehova, Kulaswa kwako kuli kosapoleka ndi bala lako lili lowawa.

13 Palibe amene adzanenera mlandu wako, ulibe mankhwala akumanga nao bala lako.

14 Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka.

15 Chifukwa chanji ulirira bala lako? Kuphwetekwa kwako kuli kosapoleka; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka, ndakuchitira iwe izi.

16 Chifukwa chake iwo akulusira iwe adzalusiridwanso; ndi adani ako onse, adzanka ku undende onsewo; ndipo iwo adzakufunkha iwe adzakhala chofunkha, ndipo onse akulanda iwe ndidzapereka kuti zilandidwe zao.

17 Pakuti ndidzakubwezera iwe moyo, ndipo ndidzapoletsa mabala ako, ati Yehova; chifukwa anatcha iwe wopirikitsidwa, nati, NdiyeZiyoni, amene kulibe munthu amfuna.

18 Atero Yehova: Taonani, ndidzabwezanso undende wa mahema a Yakobo, ndipo ndidzachitira chifundo zokhalamo zake, ndipo mzinda udzamangidwa pamuunda pake, ndi chinyumba chidzakhala momwe.

19 Ndipo padzatuluka pa izo mayamikiro ndi mau a iwo okondwerera; ndipo ndidzachulukitsa iwo, sadzakhala owerengeka; ndidzawachitiranso ulemu, sadzachepa.

20 Ana aonso adzakhala monga kale, ndipo msonkhano wao udzakhazikika pamaso panga, ndipo ndidzalanga onse amene akupsinja iwo.

21 Ndipo mkulu wao adzakhala mwa iwo, ndi wolamulira wao adzatuluka pakati pao; ndipo ndidzamyandikitsa iye, ndipo adzayandikira kwa Ine, pakuti iye wolimba mtima kuyandikira kwa Ine ndani? Ati Yehova.

22 Ndipo inu mudzakhala anthu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu.

23 Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, chatuluka, chimphepo chakukokolola: chidzagwa pamutu pa oipa.

24 Mkwiyo waukali wa Yehova sudzabwerera, mpaka wachita, mpaka watha zomwe afuna kuchita m’mtima mwake: masiku akumaliza mudzachizindikira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/30-8f3f361dedb646e2cccf0d7c429732f2.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *