Yeremiya atsutsana ndi mneneri wonyenga, Hananiya
1 Ndipo panali chaka chomwecho, poyamba Zedekiya kukhala mfumu ya Yuda, chaka chachinai, mwezi wachisanu, kuti Hananiya mwana wa Azurimneneri, amene anali wa ku Gibiyoni, ananena ndi ine m’nyumba ya Yehova, pamaso pa ansembe ndi pa anthu onse, kuti,
2 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, kuti, Ndathyola goli la mfumu ya ku Babiloni.
3 Zisanapite zaka ziwiri zamphumphu Ine ndidzabwezeranso kumalo kuno zipangizo zonse za m’nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anazichotsa muno, kunka nazo ku Babiloni;
4 ndipo ndidzabwezeranso kumalo kuno Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi am’nsinga onse a Yuda, amene ananka ku Babiloni, ati Yehova: pakuti ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babiloni.
5 Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa Hananiya mneneri pamaso pa ansembe, ndi pamaso pa anthu onse amene anaima m’nyumba ya Yehova,
6 Yeremiya mneneri anati, Amen: Yehova achite chotero: Yehova atsimikize mau ako amene wanenera, abwezerenso zipangizo za nyumba ya Yehova, ndi onse amene anachotsedwa am’nsinga, kuchokera ku Babiloni kudza kumalo kuno.
7 Koma mumvetu mau awa amene ndinena m’makutu anu, ndi m’makutu a anthu onse:
8 Aneneri amene analipo kale ndisanakhale ine, nimusanakhale inu, ananenera maiko ambiri, ndi mafumu aakulu, za nkhondo, ndi za choipa, ndi za mliri.
9 Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzachitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu.
10 Pamenepo mneneri Hananiya anachotsa goli pa khosi la Yeremiya, nalithyola.
11 Ndipo Hananiya ananena pamaso pa anthu onse, kuti, Yehova atero: Chomwecho ndidzathyola goli la Nebukadinezara mfumu ya Babiloni zisanapite zaka ziwiri zamphumphu kulichotsa pa khosi la amitundu onse. Ndipo Yeremiya mneneri anachoka.
12 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, atathyola Hananiya mneneri goli kulichotsa pa khosi la Yeremiya, kuti,
13 Pita, nunene kwa Hananiya, kuti Yehova atero: Wathyola magoli amtengo; koma udzapanga m’malo mwao magoli achitsulo.
14 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Ndaika goli lachitsulo pa khosi la amitundu onsewa, kuti amtumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo adzamtumikira iye; ndipo ndampatsanso nyama zakuthengo.
15 Ndipo Yeremiya mneneri ananena kwa Hananiya mneneri, Tamvatu, Hananiya; Yehova sanakutume iwe; koma ukhulupiritsa anthu awa zonama.
16 Chifukwa chake Yehova atero, Taona, Ine ndidzakuchotsa iwe kudziko; chaka chino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova.
17 Ndipo anafa Hananiya mneneri chaka chomwecho mwezi wachisanu ndi chiwiri.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/28-96111d6c19129eab8dfd1f8441622ff4.mp3?version_id=1068—