1 Yehova atero: Tsikira kunyumba ya mfumu ya Yuda, ndi kunena komweko mau awa,
2 ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi.
3 Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m’dzanja la wosautsa; musachite choipa, musamchitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano.
4 Pakuti ngati mudzachitadi ichi pamenepo, padzalowa pa zipata za nyumba iyi mafumu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera m’magaleta ndi pa akavalo, iye, ndi atumiki ake, ndi anthu ake.
5 Koma ngati simudzamva mau amenewa, Ine ndilumbira, pali Ine mwini, ati Yehova, nyumba iyi idzakhala yabwinja.
6 Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Giliyadi, ndi mutu wa Lebanoni; koma ndidzakuyesa iwe chipululu, ndi mizinda yosakhalamo anthu.
7 Ndipo ndidzakupangiratu iwe opasula, yense ndi zida zake; ndipo adzadula mikungudza yako yosankhika nadzaiponya m’moto.
8 Ndipoamitunduambiri adzapita pa mzinda uwu, nadzati yense kwa mnzake, Yehova anatero nao mzinda waukulu uwu chifukwa ninji?
9 Ndipo adzayankha, Chifukwa anasiya pangano la Yehova Mulungu wao, ndi kugwadira milungu ina, ndi kuitumikira.
10 Musamlirire wakufa, musachite maliro ake; koma mumliritse iye amene amuka, pakuti sadzabweranso, kapena kuonanso dziko la kwao.
11 Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m’malo mwake mwa Yosiya atate wake, amene anatuluka m’malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iliyonse;
12 koma kumene anamtengera iye ndende, kumeneko adzafa, ndipo sadzaonanso dziko ili.
13 Tsoka iye amene amanga nyumba yake ndi chisalungamo, ndi zipinda zapamwamba ndi chosaweruza bwino; amene agwiritsa mnzake ntchito osamlipira, osampatsa mphotho yake;
14 amene ati, Ndidzadzimangira ndekha nyumba yotakata ndi zipinda zapamwamba zazikulu, nadziboolera mazenera; navundikira tsindwi lam’kati ndi mikungudza, naipaka ndi utoto wofiira.
15 Kodi udzakhala mfumu, chifukwa iwe uyesa kuposa ena ndi mikungudza? Kodi atate wako sanadye ndi kumwa, ndi kuweruza molungama? Kumeneko kunamkomera.
16 Iye anaweruza mlandu wa aumphawi ndi osowa; kumeneko kunali kwabwino. Kodi kumeneko si kundidziwa Ine? Ati Yehova.
17 Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite.
18 Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda: Sadzamlira iye, kuti, Kalanga ine mbale wanga! Kapena, Kalanga ine mlongo wanga! Sadzamlira, kuti, Kalanga ine mbuye! Kapena, Kalanga ine ulemerero wake!
19 Adzamuika monga kuika bulu, adzamkoka nadzamponya kunja kwa zipata zaYerusalemu.
20 Kwera ku Lebanoni, nufuule; kweza mau ako mu Basani; nufuule mu Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha.
21 Ndinanena ndi iwe m’phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvere mau anga.
22 Mphepo idzadyetsa abusa ako onse, ndipo mabwenzi ako adzalowa m’ndende; ntheradi udzakhala ndi manyazi ndi kunyazitsidwa chifukwa cha choipa chako chonse.
23 Iwe wokhala mu Lebanoni, womanga chisa chako m’mikungudza, udzachitidwa chisoni chachikulu nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!
24 Pali Ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wake wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya padzanja langa lamanja, ndikadachotsa iwe kumeneko;
25 ndipo ndidzakupereka iwe m’dzanja la iwo amene afuna moyo wako, m’dzanja la iwo amene uwaopa, m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, m’dzanja la Ababiloni.
26 Ndipo ndidzakutulutsa iwe, ndi mai wako wakubala iwe, kulowa m’dziko lina, limene sunabadwiremo; m’menemo udzafa.
27 Koma kudziko kumene moyo wao ukhumba kubwerera, kumeneko sadzabwerako.
28 Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? Chifukwa chanji atulutsidwa iye, ndi mbeu zake, ndi kuponyedwa m’dziko limene salidziwa?
29 Iwe dziko, dziko, dziko lapansi, tamvera mau a Yehova.
30 Atero Yehova, Lembani munthu uyu wopanda ana, munthu wosaona phindu masiku ake; pakuti palibe munthu wa mbeu zake adzaona phindu, ndi kukhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi kulamuliranso mu Yuda.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/22-be03f905051d5fcc470d12846f260479.mp3?version_id=1068—