Fanizo la mpango wabafuta lifanizira kulangidwa kwao
1 Atero Yehova kwa ine, Pita, udzigulire mpango wabafuta, nudzimangire m’chuuno mwako, usauike m’madzi.
2 Ndipo ndinagula mpango monga mwa mau a Yehova, ndi kuvala m’chuuno mwanga.
3 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yachiwiri, kuti,
4 Tenga mpango umene unaugula, umene uli m’chuuno mwako, nuuke, nupite ku Yufurate, nuubise m’menemo m’phanga la m’mwala.
5 Ndipo ndinapita, ndinaubisa pa Yufurate, monga Yehova anandiuza ine.
6 Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati kwa ine, Uka, pita ku Yufurate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko.
7 Ndipo ndinanka ku Yufurate, ndikukumba, nditenga mpango m’malo m’mene ndinaubisamo; ndipo, taonani, mpango unaonongeka, wosayenera kanthu.
8 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,
9 Yehova atero, Momwemo ndidzaononga kudzitama kwa Yuda, ndi kudzitama kwakukulu kwaYerusalemu.
10 Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m’kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.
11 Pakuti monga mpango uthina m’chuuno cha munthu, chomwecho ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israele ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi chilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva.
12 Chifukwa chake uzinena ndi iwo mau awa: Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo; ndipo adzati kwa iwe, Kodi sitidziwitsa bwino kuti matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo?
13 Ndipo udzati kwa iwo, Atero Yehova, Taonani, ndidzadzaza ndi chiledzero onse okhala m’dziko muno, ngakhale mafumu onse amene akhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi onse okhala mu Yerusalemu.
14 Ndipo ndidzaphwanyanitsa wina ndi wina, atate ndi ana, ati Yehova; sindidzakhala ndi chisoni, sindidzapulumutsa, sindidzakhala ndi chifundo, chakuti ndisawaononge.
15 Tamvani inu, Tcherani khutu; musanyade, pakuti Yehova wanena.
16 Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanaphunthwe pa mapiri achizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Iye asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii.
17 Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m’tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m’nsinga.
18 Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.
19 Mizinda ya kumwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda yense wachotsedwa m’ndende yenseyo, wachotsedwa m’nsinga.
20 Tukulani maso anu, taonani iwo amene achokera kumpoto; zili kuti zoweta zinapatsidwa kwa iwe, zoweta zako zokoma?
21 Udzanena chiyani pamene adzaika abale ako kukhala akulu ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? Kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala?
22 Ndipo ngati udzati m’mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine chifukwa ninji? Chifukwa cha choipa chako chachikulu nsalu zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zitendene zako zaphwetekwa.
23 Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lake, kapena nyalugwe mawanga ake? Pamenepo mungathe inunso kuchita zabwino, inu amene muzolowera kuchita zoipa.
24 Chifukwa chake ndidzabalalitsa iwo, monga ziputu zakupita, ndi mphepo ya kuchipululu.
25 Ichi ndi chogwera chako, gawo la muyeso wako wa kwa Ine, ati Yehova; chifukwa wandiiwala Ine, ndi kukhulupirira zonama.
26 Chifukwa chake Ine ndidzaonetsa zotopola mikawo zako, pamaso pako, ndipo manyazi ako adzaoneka.
27 Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m’munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/13-8ee6bba6039d2b9c06aa75be9d77a9f5.mp3?version_id=1068—