Categories
YAKOBO

YAKOBO 5

Achuma ouma mtima atsutsidwa

1 Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu.

2 Chuma chanu chaola ndi zovala zanu zajiwa ndi njenjete.

3 Golide wanu ndisilivawanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza.

4 Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m’minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m’makutu a Ambuye wa makamu.

5 Mwadyerera padziko, ndipo mwachita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m’tsiku lakupha.

6 Munamtsutsa, munapha wolungamayo, iye sakaniza inu.

Apirire. Za kulumbira, kupemphera, kubweza wosochera

7 Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya chizimalupsa ndi masika.

8 Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira.

9 Musaipidwe wina ndi mnzake, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo.

10 Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m’dzina la Ambuye.

11 Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.

12 Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m’chiweruziro.

13 Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire.

14 Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu aMpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la Ambuye:

15 ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.

16 Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m’machitidwe ake.

17 Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwe mvula padziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi.

18 Ndipo anapempheranso; ndipo m’mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake.

19 Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake;

20 azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa kunjira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzavundikira machimo aunyinji.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JAS/5-ff1832cb27ea435e04dd90535a98e3ac.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *