Azichenjera ndi pakamwa pao
1 Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa.
2 Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.
3 Koma ngati tiikira akavalo zogwirira m’kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao lonse.
4 Taonani, zombonso, zingakhale zazikulu zotere, nkutengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigiro laling’ono ndithu kumene kulikonse afuna wogwira tsigiro.
5 Kotero lilimenso lili chiwalo chaching’ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang’ono kayatsa nkhuni zambiri!
6 Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndiGehena.
7 Pakuti mtundu uliwonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam’nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zazoloweretsedwa ndi anthu;
8 koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; lili choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.
9 Timayamika Ambuye ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu;
10 Mochokera m’kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.
11 Kodi kasupe atulutsira pa uno womwewo madzi okoma ndi owawa?
12 Kodi mkuyu ukhoza kubalaazitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sangathe kutulutsa okoma.
Nzeru yochokera Kumwamba
13 Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.
14 Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m’mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi.
15 Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya ziwanda.
16 Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi chochita choipa chilichonse.
17 Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.
18 Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JAS/3-91e9b88f1bda5bdcf04695d91b72bb18.mp3?version_id=1068—