Abimeleki awapha abale ake
1 Koma Abimeleki mwana wa Yerubaala anamuka ku Sekemu kwa abale a amai wake, nanena nao, ndi kwa banja lonse la nyumba ya atate wa amai wake, ndi kuti,
2 Nenanitu m’makutu mwa eni ake onse a ku Sekemu, Chokomera inu nchiti, akulamulireni ana aamuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? Mukumbukirenso kuti ine ndine wa fuko lanu ndi nyama yanu.
3 Pamenepo abale a amake anamnenera mau awa onse m’makutu a eni ake onse a Sekemu; ndi mitima yao inalunjika kutsata Abimeleki; pakuti anati, Ndiye mbale wathu.
4 Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m’nyumba ya Baala-Beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pake ndi opepuka amene anamtsata.
5 Ndipo anamuka kunyumba ya atate wake ku Ofura, nawapha abale ake ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng’ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.
6 Pamenepo anasonkhana eni ake onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa choimiritsa chili mu Sekemu.
Fanizo la Yotamu
7 Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu paphiri la Gerizimu, nakweza mau ake, nafuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ake a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu.
8 Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu; niti kwa mtengo waazitona, Ukhale iwe mfumu yathu.
9 Koma mtengo wa azitona unati kwa iwo, Ngati ndidzasiya kunona kwanga kumene alemekeza nako Mulungu ndi anthu kukalenga pa mitengo?
10 Pamenepo mitengo inati kwa mkuyu. Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.
11 Koma mkuyu unanena nao, Ngati ndidzasiya kuzuna kwanga, ndi zipatso zanga zokoma kukalenga pa mitengo?
12 Pamenepo mitengo inati kwa mpesa, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.
13 Koma mpesa unanena nao, Ngati ndidzasiya vinyo wanga wakusekeretsa Mulungu ndi anthu, kukalenga pa mitengo?
14 Pamenepo mitengo yonse inati kwa nkandankhuku, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.
15 Ndipo nkandankhuku unati kwa mitengo, Mukandidzoza mfumu yanu moonadi, tiyeni, thawirani ku mthunzi wanga; mukapanda kutero utuluke moto m’nkandankhuku ndi kunyeketsa mikungudza ya Lebanoni.
16 Ndipo tsopano, ngati mwachita moona ndi mwangwiro pakulonga Abimeleki ufumu, ngatinso mwamchitira chokoma Yerubaala ndi nyumba yake, ndi kumchitira monga anayenera manja ake;
17 pakuti atate wanga anakugwirirani nkhondo, nataya moyo wake, nakupulumutsani m’dzanja la Amidiyani;
18 koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ake, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wake, akhale mfumu ya pa eni ake a ku Sekemu, chifukwa ali mbale wanu;
19 ngati tsono mwachitira Yerubaala ndi nyumba yake zoona ndi zangwiro lero lino, kondwerani naye Abimeleki, nayenso akondwere nanu;
20 koma ngati simunatero, utuluke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ake a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nutuluke moto kwa eni ake a ku Sekemu, ndi kunyumba yake ya Milo, nunyeketse Abimeleki.
21 Pamenepo Yotamu anafulumira, nathawa, namuka ku Beere, nakhala komweko, chifukwa cha Abimeleki mbale wake.
Mpanduko wa Gaala
22 Abimeleki atakhala kalonga wa Israele zaka zitatu,
23 Mulungu anatumiza mzimu woipa pakati pa Abimeleki ndi eni ake a ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamchitira Abimeleki mosakhulupirika;
24 kuti chiwawa adachitira ana aamuna makumi asanu ndi awiri a Yerubaala chimdzere, ndi kuti mwazi wao uikidwe pa mbale wao Abimeleki anawaphayo, ndi pa eni ake a ku Sekemu, amene analimbikitsa manja ake, awaphe abale ake.
25 Ndipo eni ake a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki.
26 Ndipo Gaala, mwana wa Ebedi anadza ndi abale ake, napita ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamkhulupirira.
27 Ndipo anatuluka kunka kuminda, natchera mphesa m’mindamo, naponda mphesa, napereka nsembe yolemekeza, nalowa m’nyumba ya mulungu wao, nadya, namwa, natemberera Abimeleki.
28 Pamenepo Gaala, mwana wa Ebedi anati, Abimeleki ndani, ndi Sekemu ndani, kuti timtumikire? Sindiye mwana wa Yerubaala kodi? Ndi Zebuli kazembe wake? Mutumikire amuna a Hamori atate wa Sekemu; koma ameneyo timtumikire chifukwa ninji?
29 Mwenzi anthu awa akadakhala m’dzanja langa; ndikadamchotsadi Abimeleki. Ndipo anati kwa Abimeleki, Chulukitsa khamu lako, nutuluke.
30 Pamene Zebuli woyang’anira mzinda anamva mau a Gaala mwana wa Ebedi, anapsa mtima.
31 Natuma mithenga kwa Abimeleki ku Aruma monyenga nati, Taonani Gaala mwana wa Ebedi ndi abale ake afika ku Sekemu; ndipo taonani, akupandukitsirani mzinda.
32 Ndipo tsopano, taukani usiku, inu ndi anthu okhala nanu ndi kulalira kuthengo;
33 ndipo kukhale kuti m’mawa, pakutuluka dzuwa, muuke mamawa mugwere mzindawo; ndipo taonani, akakutulukirani iye ndi anthu ali naye, uzimchitira monga lidziwa dzanja lako.
34 Pamenepo Abimeleki anauka ndi anthu onse anali naye, usiku; nalalira a ku Sekemu, magulu anai.
35 Ndipo Gaala mwana wa Ebedi anatuluka, naima polowera pa chipata cha mzinda; naika Abimeleki ndi anthu anali naye m’molalira.
36 Ndipo pamene Gaala anapenya anthuwo anati kwa Zebuli, Taona, alikutsika anthu kuchokera pamwamba pa mapiri. Koma Zebuli ananena naye, Uona mthunzi wa mapiri ndi kuyesa anthu.
37 Koma Gaala ananenanso, nati, Tapenya alikutsika anthu pakati padziko, ndi gulu limodzi lidzera njira ya ku thundu wa alauli.
38 Pamenepo Zebuli anati kwa iye, Pakamwa pako mpoti tsopano, muja udanena, Ndani Abimeleki kuti timtumikire? Awa si anthuwo unawapeputsa? Utuluke tsopano, nulimbane nao.
39 Ndipo Gaala anatuluka pamaso pao pa eni ake a ku Sekemu, nalimbana ndi Abimeleki.
40 Koma Abimeleki anampirikitsa, nathawa iye pamaso pake; nagwa olasidwa ambiri mpaka polowera pa chipata.
41 Ndipo Abimeleki anakhala ku Aruma; ndi Zebuli anaingitsa Gaala ndi abale ake kuti asakhale mu Sekemu.
42 Ndipo kunali m’mawa mwake, kuti anthu anatuluka kunka kuminda; ndipo anauza Abimeleki.
43 Pamenepo anatenga anthu, nawagawa magulu atatu, nalalira m’minda; napenya, ndipo taonani, anthu alimkutuluka m’mzinda; nawaukira iye nawakantha.
44 Ndi Abimeleki ndi magulu okhala naye anathamanga naima polowera pa chipata cha mzinda; ndi magulu awiriwo anagwera onse okhala m’munda, nawakantha.
45 Ndipo Abimeleki analimbana ndi mzinda tsiku lija lonse; nalanda mzinda nawapha anthu anali m’mwemo; napasula mzinda; nawazapo mchere.
46 Ndipo pamene eni ake onse a Nsanja ya ku Sekemu anachimva, analowa m’ngaka ya nyumba ya Eliberiti.
47 Ndipo anauza Abimeleki kuti amuna onse a Nsanja ya ku Sekemu asonkhana.
48 Pamenepo Abimeleki anakwera kunka kuphiri la Zalimoni, iye ndi anthu onse anali naye; natenga nkhwangwa m’dzanja lake Abimeleki, nadula nthambi kumitengo, nainyamula ndi kuiika paphewa pake, nati kwa anthu okhala naye, Ichi munachiona ndachita, fulumirani, muchite momwemo.
49 Ndi anthu onse anadulanso yense nthambi yake, natsata Abimeleki, naziika pangaka, natentha nazo ngakayo ndi moto; motero anthu onse a Nsanja ya ku Sekemu anafanso, amuna ndi akazi ngati chikwi chimodzi.
Imfa ya Abimeleki
50 Pamenepo Abimeleki anamuka ku Tebezi, naumangira Tebezi misasa, naulanda.
51 Koma m’mzindamo munali nsanja yolimba nathawira kumeneko amuna ndi akazi onse, ndi eni ake onse a mzindawo, nadzitsekereza m’mwemo, nakwera patsindwi pa nsanja.
52 Ndipo Abimeleki anafika kunsanja, nalimbana nayo nkhondo, nayandikira kukhomo kwa nsanja, aitenthe ndi moto.
53 Ndipo mkazi wina anaponya mwala wa mphero pamutu pa Abimeleki, naphwanya bade lake.
54 Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.
55 Pamene amuna a Israele anaona kuti adafa Abimeleki anamuka yense kumalo kwake.
56 Momwemo Mulungu anambwezera Abimeleki choipacho anachitira atate wake ndi kuwapha abale ake makumi asanu ndi awiri.
57 Ndipo Mulungu anawabwezera choipa chonse cha amuna a ku Sekemu pamitu pao, ndipo linawagwera temberero la Yotamu mwana wa Yerubaala.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/9-3a3ca7324ffff31ab209fdb44f2633d1.mp3?version_id=1068—