Categories
OWERUZA

OWERUZA 4

Debora ndi Baraki alanditsa Aisraele m’dzanja la Yabini

1 Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, atafa Ehudi.

2 Ndipo Yehova anawagulitsa m’dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wochita ufumu ku Hazori; kazembe wake wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti waamitundu.

3 Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.

4 Ndipo Debora,mneneriwamkazi, ndiye mkazi wake wa Lapidoti, anaweruza Israele nyengo ija.

5 Ndipo anakhala patsinde pa mgwalangwa wa Debora pakati pa Rama ndi Betele ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anakwera kwa iye awaweruze.

6 Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinowamu, achoke mu Kedesi-Nafutali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israele sanalamulire ndi kuti, Muka, nulunjike kuphiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafutali ndi ana a Zebuloni?

7 Ndipo ndidzamkoka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere ku mtsinje wa Kisoni, ndi magaleta ake, ndi aunyinji ake; ndipo ndidzampereka m’dzanja lako.

8 Ndipo Baraki anati kwa iye, Ukamuka nane, ndidzamuka; ukapanda kumuka nane, sindimuka.

9 Nati iye, Kumuka ndidzamuka nawe, koma ulendo umukawo, sudzachita nao ulemu; pakuti Yehova adzagulitsa Sisera m’dzanja la mkazi. Motero Debora anauka namuka ndi Baraki ku Kedesi.

10 Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafutali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kunka naye.

11 Ndipo Hebere Mkeni anadzisiyanitsa ndi Akeni, ndi ana a Hobabu mlamu wake wa Mose, namanga mahema ake mpaka thundu wa mu Zaananimu, ndiwo wa ku Kedesi.

12 Ndipo anauza Sisera kuti Baraki mwana wa Abinowamu wakwera kuphiri la Tabori.

13 Pamenepo Sisera anasonkhanitsa magaleta ake onse ndiwo magaleta mazana asanu ndi anai achitsulo, ndi anthu onse okhala naye, kuyambira Haroseti wa amitundu mpaka mtsinje wa Kisoni.

14 Ndipo Debora anati kwa Baraki, Nyamuka; pakuti ili ndi tsikuli Yehova wapereka Sisera m’dzanja lako; sanatuluke kodi Yehova pamaso pako? Potero Baraki anatsika kuphiri la Tabori ndi amuna zikwi khumi akumtsata.

15 Ndipo Yehova anaononga Sisera ndi magaleta onse ndi gulu lankhondo lonse, ndi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagaleta nathawa choyenda pansi.

16 Koma Baraki anatsata magaleta ndi gululo mpaka Haroseti wa amitundu; ndi gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa, sanatsale munthu ndi mmodzi yense.

17 Koma Sisera anathawira choyenda pansi ku hema wa Yaele mkazi wa Hebere Mkeni; pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori, ndi nyumba ya Hebere Mkeni.

18 Ndipo Yaele anatuluka kukomana ndi Sisera, nanena naye, Patuka, mbuye wanga, patukira kwa ine kuno; usaope. Ndipo anapatukira kwa iye kulowa m’hema, namfunda ndi chimbwi.

19 Pamenepo ananena naye, Ndipatsetu madzi pang’ono ndimwe; popeza ndine waludzu. Ndipo anatsegula thumba la mkaka, nampatsa amwe, namfunda.

20 Ndipo Sisera ananena naye, Taima pakhomo pa hema, ndipo kudzali, akadza munthu, akakufunsa akati, Pali munthu pano kodi? Uziti, Palibe.

21 Pamenepo Yaele mkazi wa Hebere anatenga chichiri cha hema, natenga nyundo m’dzanja lake namdzera monyang’ama, nakhomera chichiri chilowe m’litsipa mwake; ndipo chinapyoza kulowa m’nthaka; popeza anali m’tulo tofa nato ndi kulema; nafa.

22 Ndipo taonani, pomlondola Sisera Barakiyo, Yaele anatuluka kukomana naye, nati kwa iye, Idza kuno, ndidzakuonetsa munthu umfunayo. Potero anamdzera, ndipo taonani, Sisera wagwa, wafa, ndi chichiri m’litsipa mwake.

23 Momwemo Mulungu anagonjetsa tsiku lija Yabini mfumu ya Kanani pamaso pa ana a Israele.

24 Ndipo dzanja la ana a Israele linankabe ndi kulimbika pa Yabini mfumu ya Kanani mpaka adamuononga Yabini mfumu ya Kanani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/4-6c3dd0c90a55cbda0d7382cc4f081d51.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *