Fuko la Benjamini limangidwanso
1 Koma amuna a Israele adalumbira ku Mizipa, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzapereka mwana wake wamkazi kwa Mbenjamini akhale mkazi wake.
2 Ndipo anthu anadza ku Betele, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri.
3 Nati iwo, Yehova Mulungu wa Israele, chachitika ichi chifukwa ninji mu Israele, kuti lasowa lero fuko limodzi mu Israele?
4 Ndipo kunali m’mawa mwake, anthu analawirira mamawa namangako guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika.
5 Nati ana a Israele, Ndani iye mwa mafuko onse a Israele amene sanakwere kudza kumsonkhano kwa Yehova? Pakuti panali lumbiro lalikulu pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu.
6 Ndipo ana a Israele anamva chifundo chifukwa cha Benjamini mbale wao, nati, Fuko limodzi lalikhidwa pa Israele leroli.
7 Tidzatani kuwafunira otsalawo akazi, popeza tinalumbira ife pa Yehova kuti sitidzawapatsa ana athu aakazi akhale akazi ao?
8 Nati iwo, Kodi pali lina la mafuko a Israele losakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa? Ndipo taonani, kuchokera ku Yabesi-Giliyadi sanadze mmodzi kumisasa, kumsonkhano.
9 Pakuti pamene anawerenga anthu, taonani, panalibe mmodzi komweko wa okhala mu Yabesi-Giliyadi.
10 Ndipo msonkhano unatumizako amuna zikwi khumi ndi ziwiri, ndiwo ngwazi, nawalamulira ndi kuti, Mukani, nimuwakanthe okhala mu Yabesi-Giliyadi ndi lupanga lakuthwa, ndi akazi ndi ana aang’ono.
11 Ndipo chimene mukachite ndi ichi: mukaononge konse mwamuna aliyense, ndi mkazi aliyense wodziwa mwamuna mogona naye.
12 Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-Giliyadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m’dziko la Kanani.
13 Ndipo msonkhano wonse unatumiza mau kwa ana a Benjamini okhala m’thanthwe la Rimoni, nawalalikira mtendere.
14 Nakwera Abenjamini nthawi ija, ndipo anawapatsa akazi amene anawasunga amoyo mwa akazi a Yabesi-Giliyadi; koma sanawafikire.
15 Ndipo anthu anamva chifundo pa Benjamini, pakuti Yehova adang’amba mafuko a Israele.
16 Pamenepo akulu a msonkhano anati, Tidzatani, kuwafunira akazi otsalawo, popeza akazi anatha psiti mu Benjamini?
17 Nati iwo, Pakhale cholowa cha iwo opulumuka a Benjamini, lingafafanizidwe fuko mu Israele.
18 Koma ife sitingathe kuwapatsa ana athu aakazi akhale akazi ao; pakuti ana a Israele adalumbira ndi kuti, Atembereredwe wakupatsa Abenjamini mkazi.
19 Nati iwo, Taonani, pali madyerero a Yehova chaka ndi chaka ku Silo, ndiko kumpoto kwa Betele, kum’mawa kwa mseu wokwera kuchokera ku Betele kunka ku Sekemu, ndi kumwera kwa Lebona.
20 Ndipo analamulira ana a Benjamini ndi kuti, Mukani, mulalire m’minda yampesa;
21 nimuyang’ane, ndipo taonani, atatuluka ana aakazi a Silo kuvinavina, pamenepo mutuluke m’minda yampesa ndi kudzigwirira yense mkazi wake mwa ana aakazi a Silo, ndi kumuka naye ku dziko la Benjamini.
22 Ndipo kudzali, akatifikira atate ao kapena alongo ao kunena nafe mlandu, tidzanena nao, Mutipatse awa, pakuti sitinawatengera yense mkazi wake kunkhondo; pakuti inunso simunawaninkhe awa; mukadatero mukadapalamula tsopano.
23 Nachita chotere ana a Benjamini, nadzitengera akazi monga mwa kuwerenga kwao, a ovina aja, amene anawatenga mwachifwamba; namuka iwo nabwerera ku cholowa chao, namanga midzi, nakhalamo.
24 Ndipo ana a Israele anachokako nthawi ija yense kunka ku fuko lake, ndi banja lake, natulukako yense kunka ku cholowa chake.
25 Panalibe mfumu mu Israele masiku aja; yense anachita chomkomera pamaso pake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/21-d2e034550e44b4aaab9af4ec430846a9.mp3?version_id=1068—