Categories
OWERUZA

OWERUZA 16

Samisoni ku Gaza

1 Ndipo Samisoni anamuka ku Gaza, naonako mkazi wadama, nalowana naye.

2 Koma wina anauza a ku Gaza, ndi kuti, Samisoni walowa kuno. Pamenepo anamzinga, namlalira usiku wonse pa chipata cha mzinda, nakhala chete usiku wonse ndi kuti, Tidikire mpaka kucha, pamenepo tidzamupha.

3 Koma Samisoni anagona mpaka pakati pa usiku, nauka pakati pa usiku, nagwira zitseko za pa chipata cha mzinda, ndi mphuthu ziwirizo, nazichotsa ndi mpiringidzo womwe, naziika pa mapewa ake, nakwera nazo pamwamba paphiri lili pandunji pa Hebroni.

Delila apereka Samisoni

4 Ndipo pambuyo pake kunali kuti anakonda mkazi m’chigwa cha Soreki, dzina lake ndiye Delila.

5 Ndipo akalonga a Afilisti anamkwerera mkaziyo, nanena naye, Umkope nuone umo muchokera mphamvu yake yaikulu, ndi umo tingakhoze kumtha khama, kuti timmange kumzunza; ndipo tidzakupatsa aliyense ndalama mazana khumi ndi limodzi.

6 Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Ndikupempha, undiuze umo muchokera mphamvu yako yaikulu, ndi chimene angakumange nacho, kuti akuzunze.

7 Nanena naye Samisoni, Akandimanga nazo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma, ndidzakhala wofooka, wakunga munthu wina.

8 Pamenepo akalonga a Afilisti anakwera nazo kwa mkaziyo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma; ndipo iye anammanga nazo.

9 Koma anali nao omlalira m’chipinda cha m’kati. Nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Pamenepo anadula nsingazi, monga iduka m’khosi yathonje pokhudza moto. M’mwemo mphamvu yake siinadziwike.

10 Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Taona, wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze tsopano, ndikupempha, chimene angakumange nacho.

11 Nanena naye, Akandimangitsa nazo zingwe zatsopano, zosagwira nazo ntchito pamenepo ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina.

12 Ndipo Delila anatenga nsinga zatsopano, nammanga nazo, nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Ndi omlalira analikulinda m’chipinda cha m’kati. Koma anazidula pa manja ake ngati thonje.

13 Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Mpaka tsopano wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze chimene angakumange nacho. Nanena naye, Ukaomba njombi zisanu ndi ziwiri za pamutu panga mwa thonje loyala ndiko.

14 Ndipo anachimanga ndi phanga, nati kwa iye, Akugwera Afilisti, Samisoni; nagalamuka iye patulo take, nazula phanga la pamtanda, ndi thonje loyala lomwe.

15 Pamenepo ananena naye, Ukati bwanji, Ndikukonda, osamvana nane mtima wako? Wandipusitsa katatu tsopano, osandiuza umo muchokera mphamvu yako yaikulu.

16 Ndipo kunali, popeza anamuumiriza masiku onse ndi mau ake, namkakamiza, moyo wake unavutika nkufuna kufa.

17 Pomwepo anamfotokozera mtima wake wonse, nanena naye, Pamutu panga sipanapite lumo, pakuti ndineMnaziriwa Mulungu chiyambire mimba ya mai wanga; akandimeta, mphamvu yanga idzandichokera, ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina aliyense.

18 Ndipo pamene Delila anaona kuti adamfotokozera mtima wake wonse, anatuma naitana akalonga a Afilisti, ndi kuti, Kwerani nthawi ino, pakuti wandifotokozera za mtima wake wonse. Nakwera akalonga a Afilisti nadza kwa iye nabwera nazo ndalamazo m’dzanja lao.

19 Pamenepo anamgonetsa pa mabondo ake, naitana munthu, nameta njombi zake zisanu ndi ziwiri; nayamba kumzunza, nimchokera mphamvu yake.

20 Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samisoni. Nagalamuka iye m’tulo take, nati, Ndizituluka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwe kuti Yehova adamchokera.

21 Pamenepo Afilisti anamgwira, namkolowola maso, natsika naye ku Gaza, nammanga ndi maunyolo amkuwa; namperetsa m’kaidi.

22 Koma atammeta tsitsi la pamutu pake linayamba kumeranso.

Samisoni agwetsa nyumba ya Dagoni, namwalira

23 Ndipo anasonkhana akalonga a Afilisti kuperekera Dagoni mulungu wao nsembe yaikulu, ndi kusekerera; pakuti anati, Mulungu wathu wapereka Samisoni mdani wathu m’dzanja lathu.

24 Ndipo pakumuona anthu analemekeza mulungu wao, pakuti anati, Mulungu wathu wapereka m’dzanja lathu mdani wathu, ndiye wakupasula dziko lathu, amene anatiphera ambiri.

25 Ndipo kunali, pakukondwera mitima yao, anati, Kaitaneni Samisoni, atisewerere. Naitana Samisoni m’kaidi; nasewera iye pamaso pao; ndipo anamuka iye pakati pa mizati.

26 Ndipo Samisoni anati kwa mnyamata womgwira dzanja, Ndileke, ndikhudze mizati imene nyumba ikhazikikapo, kuti nditsamirepo.

27 Koma nyumbayi inadzala ndi amuna ndi akazi; ndi akalonga onse a Afilisti anali momwemo ndi patsindwi panali amuna ndi akazi ngati zikwi zitatu akuyang’ana pakusewera Samisoni.

28 Pamenepo Samisoni anaitana kwa Yehova, nati, Yehova, Mulungu, mundikumbukire, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthawi ino yokha, Mulungu, kuti ndidzilipsiriretu tsopano apa Afilisti, chifukwa cha maso anga awiri.

29 Ndipo Samisoni anagwira mizati iwiri ya pakati imene nyumba inakhazikikapo, natsamirapo wina ndi dzanja lamanja, ndi unzake ndi dzanja lamanzere.

30 Nati Samisoni, Ndife nao Afilisti; nadziweramira mwamphamvu; ndipo nyumba idagwa pa akalonga, ndi pa anthu onse anali m’mwemo. Motero akufa amene anawapha pa kufa kwake anaposa amene anawapha akali moyo.

31 Pamenepo anatsika abale ake ndi banja lonse la atate wake, namnyamula, nakwera naye, namuika pakati pa Zora ndi Esitaoli, m’manda a Manowa atate wake. Ndipo adaweruza Israele zaka makumi awiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/16-4723bcd192e2e9ec1099fbb48dad071e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *