Aisraele agonjera Afilisti; abadwa Samisoni
1 Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova; nawapereka Yehova m’dzanja la Afilisti zaka makumi anai.
2 Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lake ndiye Manowa; ndi mkazi wake analibe mwana, sanabale.
3 Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna.
4 Chifukwa chake udzisamalire, usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chinthu chilichonse chodetsa;
5 pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa MulunguMnazirichibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israele m’dzanja la Afilisti.
6 Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wake ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ake ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunse uko achokera kapena sanandiuzenso dzina lake;
7 koma anati kwa ine, Taona, udzaima, ndi kubala mwana wamwamuna; ndipo tsopano usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chilichonse chodetsa; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire mpaka tsiku la kufa kwake.
8 Pamenepo Manowa anapembedza Yehova, nati, Yehova, ndikupemphani, atidzerenso munthu wa Mulungu mudamtumayo, natilangize icho tizichitira mwanayo akadzabadwa.
9 Ndipo Mulungu anamvera mau a Manowa; ndi mthenga wa Mulungu anamdzeranso mkaziyo, pamene anali m’munda, mwamuna wake Manowa palibe.
10 Ndipo mkaziyo anafulumira nathamanga, nauza mwamuna wake, nanena naye, Taona, wandionekera munthu anandidzerayo tsiku lija.
11 Nanyamuka Manowa natsata mkazi wake, namdzera mwamuna uja, nanena naye, Kodi ndinu mwamuna uja munalankhula ndi mkaziyu? Ndipo anati, Ndine amene.
12 Nati Manowa, Achitike tsopano mau anu; koma makhalidwe ake a mwanayo ndi machitidwe ake adzatani?
13 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Zonse ndinazinena ndi mkazi azisamalire.
14 Chilichonse chichokera kumpesa asadyeko, asamwe vinyo kapena choledzeretsa, kapena kudya chilichonse chodetsa; zonse ndinamlamulira azisunge.
15 Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Tiloleni tikuchedwetseni kuti tikukonzereni mwanawambuzi.
16 Koma mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Ungakhale undichedwetsa, sindidzadya mkate wako; ndipo ukakonza nsembe yopsereza, uziipereka kwa Yehova. Pakuti Manowa sanadziwe kuti ndiye mthenga wa Yehova.
17 Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Dzina lanu ndani, kuti, atachitika mau anu, tikuchitireni ulemu.
18 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ufunsiranji dzina langa, popeza lili lodabwitsa?
19 Pamenepo Manowa anatenga mwanawambuzi pamodzi ndi nsembe yaufa, nazipereka kwa Yehova pathanthwe; ndipo mthengayo anachita modabwitsa, ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere.
20 Pakuti kunali, pakukwera lawi la moto paguwa la nsembe kumwamba, mthenga wa Yehova anakwera m’lawi la paguwalo; ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere; nagwa iwowa nkhope zao pansi.
21 Ndipo mthenga wa Yehova sanaonekerenso kwa Manowa kapena kwa mkazi wake. Pamenepo anadziwa Manowa kuti ndiye mthenga wa Yehova.
22 Nati Manowa kwa mkazi wake, Tidzafa ndithu pakuti taona Mulungu.
23 Koma mkazi wake ananena naye, Yehova akadafuna kutipha, sakadalandira nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa padzanja lathu, kapena kutionetsa izi zonse, kapena kutimvetsa zoterezi nthawi ino.
24 Ndipo mkaziyo anabala mwana wamwamuna namutcha dzina lake Samisoni; nakula mwanayo, Yehova namdalitsa.
25 Ndipo mzimu wa Yehova unayamba kumfulumiza mtima ku misasa ya Dani pakati pa Zora ndi Esitaoli.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/13-03726c0d6c23c8497e643c593cbc7fdb.mp3?version_id=1068—