Categories
OWERUZA

OWERUZA 1

Aisraele aonjeza kugonjetsa Akanani

1 Ndipo atafa Yoswa, ana a Israele anafunsira kwa Yehova ndi kuti, Adzayamba ndani kutikwerera pa Akanani kuwathira nkhondo?

2 Ndipo Yehova anati, Akwere Yuda; taonani, ndapereka dzikoli m’dzanja lake.

3 Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkulu wake, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni.

4 Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m’dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi ku Bezeki.

5 Ndipo anapeza Adoni-Bezeki mu Bezeki, namthira nkhondo nakantha Akanani ndi Aperizi.

6 Koma Adoni-Bezeki anathawa; ndipo anampirikitsa, namgwira, namdula zala zazikulu za m’manja ndi za m’mapazi.

7 Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m’manja ndi m’mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye kuYerusalemu, nafa iye komweko.

8 Ndipo ana a Yuda anachita nkhondo pa Yerusalemu, naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mzinda ndi moto.

9 Ndipo atatero ana a Yuda anatsika kuthirana nao nkhondo Akanani akukhala kumapiri, ndi kumwera ndi kuchidikha.

10 Ndipo Yuda anamuka kwa Akanani akukhala mu Hebroni; koma kale dzina la Hebroni ndilo mudzi wa Ariba; ndipo anakantha Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai.

11 Pochoka pamenepo anamuka kwa nzika za ku Debiri, koma kale dzina la Debiri ndilo mudzi wa Kiriyati-Sefere.

12 Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha mudzi wa Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake.

13 Ndipo Otiniyele, mwana wa Kenazi mng’ono wa Kalebe anaulanda, ndipo anampatsa Akisa mwana wake wamkazi akhale mkazi wake.

14 Ndipo kunali, m’mene anamdzera, anamkakamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; natsika pabulu wake; ndipo Kalebe ananena naye, Ufunanji?

15 Ndipo anati kwa iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatsenso zitsime za madzi. Pamenepo Kalebe anampatsa zitsime za kumtunda ndi zitsime za kunsi.

16 Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m’mzinda wa m’migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m’chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.

17 Ndipo Yuda anamuka ndi Simeoni mkulu wake, nakantha Akanani akukhala mu Zefati, nauononga konse. Koma dzina la mzindawo analitcha Horoma.

18 Yuda analandanso Gaza ndi malire ake, ndi Asikeloni ndi malire ake ndi Ekeroni ndi malire ake.

19 Ndipo Yehova anali ndi Yuda, iye nawaingitsa a kumapiri, osaingitsa nzika za kuchigwa, popeza zinali nao magaleta achitsulo.

20 Ndipo anapatsa Kalebe Hebroni monga Mose adanena; iye nawaingitsa komweko ana aamuna atatu a Anaki.

21 Koma ana a Benjamini sanaingitse Ayebusi okhala mu Yerusalemu; koma Ayebusi anakhala mu Yerusalemu pamodzi ndi ana a Benjamini, mpaka lero lino.

22 Ndipo anakwera iwo a m’nyumba ya Yosefe, naonso kunka ku Betele; ndipo Yehova anakhala nao.

23 Ndipo iwo a m’nyumba ya Yosefe anatumiza ozonda ku Betele. Koma kale dzina la mzindawo ndilo Luzi.

24 Ndipo alonda anaona munthu alikutuluka m’mzinda, nanena naye, Utionetsetu polowera m’mzinda, ndipo tidzakuchitira chifundo.

25 Nawaonetsa polowera m’mzinda iye, naukantha mzinda iwowa ndi lupanga lakuthwa; koma analola munthuyo ndi banja lake lonse amuke.

26 Ndipo munthuyo anamuka ku dziko la Ahiti, namanga mzinda, nautcha dzina lake Luzi; ndilo dzina lake mpaka lero lino.

Aisraele aleka kugonjetsa Akanani ena

27 Koma Manase sanaingitse a ku Beteseani ndi midzi yake kapena a Taanaki ndi midzi yake, kapena nzika za ku Dori ndi midzi yake, kapena nzika za ku Ibleamu ndi midzi yake, kapena nzika za ku Megido ndi midzi yake; koma Akanani anakhumba kukhala m’dziko muja.

28 Ndipo kunali, atakula mphamvu Israele, anasonkhetsa Akanani, osawaingitsa onse.

29 Ndipo Efuremu sanaingitse Akanani okhala mu Gezere; koma Akanani anakhala mu Gezere pakati pao.

30 Zebuloni sanaingitse nzika za ku Kitironi, kapena za ku Nahaloli; koma Akanani anakhala pakati pao, nawasonkhera.

31 Asere sanaingitse nzika za ku Ako, kapena nzika za ku Sidoni, kapena a Alabu, kapena a Akizibu, kapena a Heliba, kapena a Afiki, kapena a Rehobu;

32 koma Asere anakhala pakati pa Akanani nzika za kudziko; pakuti sanawaingitse.

33 Nafutali sanaingitse nzika za ku Betesemesi, kapena nzika za ku Betanati; koma anakhala pakati pa Akanani, nzika za kudziko; koma nzika za ku Betesemesi, ndi a ku Betanati zinawasonkhera.

34 Ndipo Aamori anakankha ana a Dani akhale kumapiri pakuti sanawalole atsikire kuchigwa;

35 Aamori anakhumbanso kukhala kuphiri la Heresi, ku Ayaloni, ndi ku Saalibimu; koma dzanja la a m’nyumba ya Yosefe linawagonjetsa, nakhala iwo akupereka msonkho.

36 Ndipo malire a Aamori anayambira pokwerera pa Akarabimu, pathanthwe ku Sela, ndi pokwererapo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/1-0ff455f23c670f97faaea4ae62cf22d5.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *