Categories
OBADIYA

OBADIYA 1

Zoipa zao ndi kulangidwa kwa Aedomu. Dalo la Israele

1 Masomphenya a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yochokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwaamitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo.

2 Taona, ndakuika wamng’ono mwa amitundu; unyozedwa kwambiri.

3 Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m’mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m’mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani?

4 Chinkana ukwera pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, chinkana chisanja chako chisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.

5 Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! Waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akutchera mphesa sadzasiya khunkha kodi?

6 Ha! Za Esau zasanthulidwa; ha! Zobisika zake zafunidwa.

7 Anthu onse a akupangana nawe anakuperekeza mpaka pamalire; anthu okhala ndi mtendere nawe anakunyenga, nakuposa mphamvu; iwo akudya chakudya chako akutchera msampha pansi pako; mulibe nzeru mwa iye.

8 Ati Yehova, Kodi sindidzaononga tsiku lija anzeru mwa Edomu, ndi luntha m’phiri la Esau?

9 Ndipo amuna anu amphamvu adzatenga nkhawa, Temani iwe, kuti onse aonongeke m’phiri la Edomu, ndi kuphedwa.

10 Chifukwa cha chiwawa unamchitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzaonongeka kunthawi yonse.

11 Tsiku lija unaima padera, tsiku lija alendo anagwira ndende makamu ake, nalowa m’zipata zake achilendo, nachitiraYerusalemumaere, iwenso unakhala ngati mmodzi wa iwowa.

12 Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka chikhakha tsiku lakupsinjika.

13 Usalowe m’mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe choipa chao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao.

14 Ndipo usaime pamphambano kuononga opulumuka ake; kapena kupereka otsala ake tsiku lakupsinjika.

15 Pakuti tsiku la Yehova layandikira amitundu onse; monga unachita iwe, momwemo adzakuchitira; chochita iwe chidzakubwerera pamutu pako.

16 Pakuti monga munamwa paphiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo.

17 Koma m’phiri laZiyonimudzakhala opulumuka, ndipo lidzakhala lopatulika; ndi a nyumba ya Yakobo adzakhala nazo zolowa zao.

18 Ndipo nyumba ya Yakobo idzakhala moto, ndi nyumba ya Yosefe lawi, ndi nyumba ya Esau ngati chiputu, ndipo adzawatentha pakati pao, ndi kuwapsereza; ndipo sadzakhalapo otsalira nyumba ya Esau; pakuti Yehova wanena.

19 Ndipo akumwera adzakhala nalo phiri la Esau cholowa chao; ndi iwo a kuchidikha adzakhala nalo dziko la Afilisti; ndipo adzakhala nayo minda ya Efuremu, ndi minda ya Samariya cholowa chao; ndi Benjamini adzakhala nalo la Giliyadi.

20 Ndipo andende a khamu ili la ana a Israele, okhala mwa Akanani, adzakhala nacho cholowa chao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala mu Sefaradi adzakhala nayo mizinda ya kumwera, cholowa chao.

21 Ndipo apulumutsi adzakwera paphiri la Ziyoni kuweruza phiri la Esau; ndipo ufumu udzakhala wake wa Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/OBA/1-b444bb72cb044c5490ac0b5d9d2212e7.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *