Categories
NYIMBO YA SOLOMONI

NYIMBO YA SOLOMONI 8

1 Mwenzi utakhala ngati mlongo wanga,

woyamwa pa bere la amai!

Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona;

osandinyoza munthu.

2 Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m’nyumba ya amai,

kuti andilange mwambo;

ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa,

ndi madzi a makangaza anga.

3 Dzanja lamanzere lake akadanditsamiritsa kumutu,

lamanja lake ndi kundifungatira.

4 Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a kuYerusalemu,

muutsiranji, mugalamutsiranji chikondi,

chisanafune mwini.

5 Ndaniyu achokera kuchipululu,

alikutsamira bwenzi lake?

Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe:

Pomwepo amai ako anali mkusauka nawe,

pomwepo wakukubala anali m’pakati pa iwe.

6 Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro,

nundikhomenso chizindikiro pamkono pako;

pakuti chikondi chilimba ngati imfa;

njiru imangouma ngati manda:

Kung’anima kwake ndi kung’anima kwa moto,

ngati mphezi ya Yehova.

7 Madzi ambiri sangazimitse chikondi,

ngakhale mitsinje yodzala kuchikokolola:

Mwamuna akapereka katundu yense wa m’nyumba yake

ngati sintho la chikondi,

akanyozedwa ndithu.

8 Tili ndi mlongo wathu wamng’ono,

alibe mawere;

timchitirenji mlongo wathu

tsiku lokhoma unkhoswe wake?

9 Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva:

Ngati ndiye chitseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza.

10 Ndine khoma, mawere anga akunga nsanja zake:

Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.

11 Solomoni anali ndi munda wamipesa ku Baala-Hamoni;

nabwereka alimi mundawo;

yense ambwezere ndalama chikwi chifukwa cha zipatso zake.

12 Koma munda wanga wamipesa,

uli pamaso panga ndiwo wangatu;

nacho chikwicho, Solomoni iwe,

koma olima zipatso zake azilandira mazana awiri.

13 Namwaliwe wokhala m’minda,

anzako amvera mau ako:

Nanenanso undimvetse.

14 Dzifulumira, mnyamatawe wokondedwa wanga,

dzifanane ngati mphoyo pena mwana wa mbawala

pa mapiri a mphoka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/SNG/8-2edcd607c87b9c7f04e8ec5a0bb46e37.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *