Categories
NYIMBO YA SOLOMONI

NYIMBO YA SOLOMONI 1

Mkwatibwi anena ndi ana a Yerusalemu za mkwati

1 Nyimbo yoposa, ndiyo ya Solomoni.

2 Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m’kamwa mwake;

pakuti chikondi chako chiposa vinyo.

3 Mafuta ako anunkhira bwino;

dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa;

chifukwa chake anamwali akukonda.

4 Undikoke; tikuthamangire;

mfumu yandilowetsa m’zipinda zake:

Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe.

Tidzatchula chikondi chako koposa vinyo:

Akukonda molungama.

5 Wakuda ine, koma wokongola,

ana aakazinu a kuYerusalemu,

ngati mahema a Kedara,

ngati nsalu zotchinga za Solomoni.

6 Musayang’ane pa ine, pakuti ndada,

pakuti dzuwa landidetsa.

Ana aamuna a amai anandikwiyira,

anandisungitsa minda yamipesa;

koma munda wangawanga wamipesa sindinausunge.

7 Ndiuze, iwe amene moyo wanga ukukonda,

umaweta kuti gulu lako?

Umaligonetsa kuti pakati pa usana?

Pakuti ndikhalirenji ngati wosochera

pambali pa magulu a anzako?

8 Ngati sudziwa, mkaziwe woposa kukongola,

dzituluka kukalondola bande la gululo,

nukawete anaambuzi zako pambali pa mahema a abusa.

Mkwati ndi mkwatibwi akambirana za chikondano chao

9 Ndakulinganiza, wokondedwa wanga mnyamatawe,

ngati akavalo a magaleta aFarao.

10 Masaya ako akongola ndi nkhata zatsitsi,

ndi khosi lako ndi zinganga za mkanda wonyezimira.

11 Tidzakupangira nkhata zagolide

ndi njumu zasiliva.

12 Pokhala mfumu podyera pake,

naridowanga ananunkhira.

13 Wokondedwa wanga mnyamatayo

ali kwa ine ngati thumba lamure,

logona pakati pa mawere anga.

14 Wokondedwa wanga ali kwa ine

ngati chipukutu cha maluwa ofiira

m’minda yamipesa ya ku Engedi.

15 Taona, wakongolatu, bwenzi langa;

namwaliwe taona, wakongola,

maso ako akunga a nkhunda.

16 Taona, wakongolatu, bwenzi langa,

mnyamatawe, inde, wakongoletsa;

pogona pathu mpa msipu.

17 Mitanda ya nyumba zathu nja mikungudza,

ndi mapaso athu nga mlombwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/SNG/1-f44648ae3302899dea72d80c85d1d64d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *