Categories
NUMERI

NUMERI 5

Odetsedwa onse achotsedwe kuchigono

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Uza ana a Israele kuti azitulutsa m’chigono akhateonse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi onse odetsedwa chifukwa cha akufa;

3 muwatulutse amuna ndi akazi muwatulutsire kunja kwa chigono, kuti angadetse chigono chao, chimene ndikhala m’kati mwakemo.

4 Ndipo ana a Israele anachita chotero, nawatulutsira kunja kwa chigono; monga Yehova adanena ndi Mose momwemo ana a Israele anachita.

Za kubwezera

5 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

6 Nena ndi ana a Israele, ndi kuti Mwamuna kapena mkazi akachita tchimo lililonse amachita anthu, kuchita mosakhulupirika pa Yehova, nakapalamuladi;

7 azivomereza tchimo lake adalichita; nabwezere chopalamulacho monsemo, naonjezeko limodzi la magawo asanu, ndi kuchipereka kwa iye adampalamulayo.

8 Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere chopalamulacho, chopalamula achibwezera Yehovacho chikhale cha wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya chotetezerapo, imene amchitire nayo chomtetezera.

9 Ndipo nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene abwera nazo kwa wansembe zisanduka zake.

10 Zopatulika za munthu aliyense ndi zake: zilizonse munthu aliyense akapatsa wansembe, zisanduka zake.

Za mlandu wa nsanje

11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

12 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mkazi wamwini akapatukira mwamuna wake, nakamchitira mosakhulupirika,

13 ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wake, ndi kumng’unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwire alimkuchita;

14 ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti achitire nsanje mkazi wake, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amchitire mkazi wake nsanje angakhale sanadetsedwe;

15 pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wake kwa wansembe, nadze nacho chopereka chake, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapolubani; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yachikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.

16 Ndipo wansembe abwere naye, namuike pamaso pa Yehova;

17 natenge madzi opatulika m’mbale yadothi wansembeyo, natengeko fumbi lili pansi mu chihema, wansembeyo nalithire m’madzimo.

18 Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m’manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m’manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.

19 Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagone nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukire kuchidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.

20 Koma iwe, ngati wapatukira mwamuna wako, ngati wadetsedwa, kuti wagona nawe munthu, wosati mwamuna wako;

21 pamenepo wansembe alumbiritse mkazi lumbiro lakutemberera, ndi wansembe anene kwa mkazi, Yehova akuike ukhale temberero ndi lumbiro pakati pa anthu a mtundu wako, pakuondetsa Yehova m’chuuno mwako, ndi kukutupitsa thupi lako;

22 ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m’matumbo mwako, nadzakutupitsa thupi lako ndi kuondetsa m’chuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti,Amen, Amen.

23 Ndipo wansembe alembere matemberero awa m’buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.

24 Ndipo amwetse mkaziyo madzi owawa akudzetsa temberero; ndi madzi odzetsa temberero adzalowa mwa iye nadzamwawira.

25 Ndipo wansembe atenge nsembe yaufa yansanje m’manja mwa mkazi, naweyule nsembe yaufa pamaso pa Yehova, nabwere nayo ku guwa la nsembe.

26 Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, chikumbutso chake, nachitenthe paguwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo.

27 Ndipo atammwetsa madziwo, kudzatero, ngati wadetsedwa, nachita mosakhulupirika pa mwamuna wake, madzi odzetsa tembererowo adzalowa mwa iye nadzamwawira, nadzamtupitsa thupi lake, ndi m’chuuno mwake mudzaonda; ndi mkaziyo adzakhala temberero pakati pa anthu a mtundu wake.

28 Koma ngati mkazi sanadetsedwe, nakhala woyera, pamenepo adzapulumuka, nadzaima.

29 Ichi ndi chilamulo cha nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wake, ampatukira nadetsedwa;

30 kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo achitira mkazi wake nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amchitire chilamulo ichi chonse.

31 Mwamunayo ndiye wosachita mphulupulu, koma mkazi uyo asenze mphulupulu yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/5-f345073e9dc6f00e3f6b266273bf68e4.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *