Mizinda ya Alevi
1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m’zidikha za Mowabu, pa Yordani, ku Yeriko, ndi kuti,
2 Uza ana a Israele, kuti apatseko Alevi cholowa chaochao, mizinda yokhalamo; muwapatsenso Alevi mabusa akuzungulira mizinda.
3 Ndipo mizinda ndiyo yokhalamo iwowa; ndi mabusa akhale a ng’ombe zao, ndi zoweta zao, inde nyama zao zonse.
4 Ndipo mabusa a mizindayo, imene muipereke kwa Alevi ndiwo a mikono chikwi chimodzi kuyambira kulinga kufikira kunja.
5 Ndipo muyese kunja kwa mzinda, mbali ya kum’mawa mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumwera mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumadzulo mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumpoto mikono zikwi ziwiri; ndi mzindawo pakati; ndiwo mabusa a kumizinda.
6 Ndipo midziyo muipereke kwa Alevi ndiyo mizinda ija isanu ndi umodzi yopulumukirako; imene muipereke kuti wakupha mnzake athawireko; ndipo pamodzi ndi iyi muperekenso midzi makumi anai ndi iwiri.
7 Midzi yonse muipereke kwa Alevi ndiyo mizinda makumi anai ndi isanu ndi itatu, iyo pamodzi ndi mabusa ao.
8 Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang’ono mutengeko pang’ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.
Mizinda yopulumukirako
9 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
10 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pakuoloka inu Yordani kulowa m’dziko la Kanani,
11 muikire mizinda ikukhalireni mizinda yopulumukirako; kuti wakupha mnzake wosati dala athawireko.
12 Ndipo mizindayo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzake asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze.
13 Ndipo mizindayo muipereke ikukhalireni mizinda isanu ndi umodzi yopulumukirako.
14 Mupereke mizinda itatu tsidya lino la Yordani, ndi mizinda itatu mupereke m’dziko la Kanani, ndiyo yopulumukirako.
15 Mizinda isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israele, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti aliyense adamupha munthu osati dala athawireko.
16 Koma akamkantha ndi chipangizo chachitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
17 Kapena akamkantha m’dzanja muli mwala, wakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
18 Kapena akamkantha m’dzanja muli chipangizo chamtengo, chakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
19 Wolipsa mwazi mwini wake aphe wakupha munthuyo; pakumpeza amuphe.
20 Ndipo akampyoza momkwiyira, kapena kumponyera kanthu momlalira, kuti wafa;
21 kapena kumpanda ndi dzanja lake momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo akampeza.
22 Koma akampyoza modzidzimuka, osamuda, kapena kumponyera kanthu osamlalira,
23 kapena kumponyera mwala wakufetsa munthu, osamuona, namgwetsera uwu, kuti wafa, koma sindiye mdani wake, kapena womfunira choipa;
24 pamenepo msonkhano uziweruza pakati pa wokantha mnzakeyo ndi wolipsa mwaziyo monga mwa maweruzo awa;
25 ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m’dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere kumzinda wake wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.
26 Koma wakupha munthu akatuluka nthawi iliyonse kulumpha malire a mzinda wake wopulumukirako kumene anathawirako;
27 nakampeza wolipsa mwazi kunja kwa malire a mzinda wake wothawirako, ndipo wolipsa mwazi akapha wakupha munthu, alibe kuchimwira mwazi;
28 popeza wakupha munthu akadakhala m’mzinda wake wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lakelake.
29 Ndipo izi zikhale kwa inu lemba la chiweruzo mwa mibadwo yanu, m’nyumba zanu zonse.
30 Aliyense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe.
31 Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, napalamula imfa; koma aziphedwa ndithu.
32 Musamalandira dipo lakuombola iye amene adathawira kumzinda wake wopulumukirako, kuti abwerenso kukhala m’dziko, kufikira atafa mkulu wa ansembe.
33 Ndipo musamaipsa dziko muli m’mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko chifukwa cha mwazi anaukhetsa m’mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.
34 Usamadetsa dziko ukhala m’mwemo, limene ndikhalitsa pakati pake; popeza Ine Yehova ndikhalitsa pakati pa ana a Israele.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/35-85538b1fe9e90870ca58db766cebc728.mp3?version_id=1068—