Aisraele agonjetsa Amidiyani
1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2 Abwezereni chilango Amidiyani chifukwa cha ana a Israele; utatero udzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wako.
3 Ndipo Mose ananena ndi anthu, nati, Adzikonzere ena mwa inu zida za nkhondo, alimbane nao Amidiyani, kuwabwezera Amidiyani chilango cha Yehova.
4 Muwatume kunkhondo a fuko limodzi, chikwi chimodzi, atere mafuko onse a Israele.
5 Ndipo anapereka mwa zikwi za Israele, a fuko limodzi chikwi chimodzi, anthu zikwi khumi ndi ziwiri okonzekeratu ndi zankhondo.
6 Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m’dzanja lake.
7 Ndipo anawathira nkhondo Amidiyani, monga Yehova adamuuza Mose; nawapha amuna onse.
8 Ndipo anapha mafumu a Amidiyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.
9 Ndipo ana a Israele anagwira akazi a Amidiyani, ndi ana aang’ono, nafunkha ng’ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi chuma chao chonse.
10 Ndipo anatentha ndi moto mizinda yao yonse yokhalamo iwo, ndi zigono zao zonse.
11 Ndipo anapita nazo zofunkha zonse, ndi zakunkhondo zonse, ndizo anthu ndi nyama.
12 Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israele, kuchigono, ku zidikha za Mowabu, zili ku Yordani pafupi pa Yeriko.
Mayeretsedwe a ankhondowo
13 Ndipo Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga onse a khamulo, anatuluka kukomana nao kunja kwa chigono.
14 Ndipo Mose anakwiya nao akazembe a nkhondoyi, atsogoleri a zikwi, atsogoleri a mazana, akufuma kunkhondo adaithira.
15 Ndipo Mose ananena nao, Kodi mwasunga ndi moyo akazi onse?
16 Taonani, awa analakwitsa ana a Israele pa Yehova ndi cha Peori chija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m’khamu la Yehova.
17 Ndipo tsono iphani amuna onse mwa anawo, iphaninso akazi onse akudziwa mwamuna mogona naye.
18 Koma ana aakazi onse osadziwa mwamuna mogona naye, asungeni ndi moyo akhale anu.
19 Ndipo mukhale m’misasa kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; aliyense adapha munthu, ndi aliyense wakukhudza wophedwa, mudziyeretse tsiku lachitatu ndi lachisanu ndi chiwiri, inu ndi andende anu.
20 Muyeretse zovala zanu zonse, zipangizo zonse zachikopa, ndi zoomba zonse za ubweya wa mbuzi, ndi zipangizo zonse za mtengo.
21 Ndipo Eleazara wansembe ananena ndi ankhondo adapita kunkhondowo, Lemba la chilamulocho Yehova analamulira Mose ndi ili:
22 Golide, ndisiliva, mkuwa, chitsulo, ndolo ndi mtovu zokha,
23 zonse zakulola moto, mupititse m’moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m’madzi.
24 Ndipo mutsuke zovala zanu tsiku lachisanu ndi chiwiri, kuti mukhale oyera; ndipo mutatero mulowe m’chigono.
Magawidwe a zofunkha
25 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
26 Werengani zakunkhondo, ndizo anthu, ndi zoweta, iwe, ndi Eleazara wansembe, ndi akulu a nyumba za makolo za khamulo;
27 nugawe zakunkhondo pawiri; pakati pa othira nkhondo amene anatuluka kunkhondo, ndi khamu lonse.
28 Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akutuluka kunkhondo apereke kwa Yehova: munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng’ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo.
29 Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.
30 Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng’ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova.
31 Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe anachita monga Yehova anamuuza Mose.
32 Ndipo zakunkhondo, zotsalira zofunkha zonse adazifunkha ankhondowa, ndizo nkhosa zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zikwi makumi asanu ndi awiri kudza zisanu,
33 ndi ng’ombe zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri,
34 ndi abulu zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu chimodzi,
35 ndi anthu, ndiwo akazi osadziwa mwamuna mogona naye, onse pamodzi zikwi makumi atatu ndi ziwiri.
36 Ndipo limodzi la magawo awiri, ndilo gawo la iwo adatuluka kunkhondo, linafikira nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu.
37 Ndi msonkho wa Yehova wankhosa ndiwo mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu.
38 Ndipo ng’ombe zidafikira zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri.
39 Ndipo abulu anafikira zikwi makumi atatu ndi mazana asanu; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi limodzi mphambu mmodzi.
40 Ndipo anthu anafikira zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo anthu makumi atatu mphambu awiri.
41 Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.
42 Ndipo kunena za gawo la ana a Israele, limene Mose adalichotsa kwa anthu ochita nkhondowo,
43 (ndipo gawo la khamulo ndilo nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu,
44 ndi ng’ombe zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi,
45 ndi abulu zikwi makumi atatu ndi mazana asanu,
46 ndi anthu zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi,)
47 mwa gawolo la ana a Israele Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
Zopereka zaufulu za akazembe
48 Pamenepo akazembe a pa ankhondo zikwi, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, anayandikiza kwa Mose;
49 nati kwa Mose, Atumiki anu anawerenga ankhondo tinali nao, ndipo sanasowe munthu mmodzi wa ife.
50 Ndipo tabwera nacho chopereka cha Yehova, yense chimene anachipeza, zokometsera zagolide, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kuchita chotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.
51 Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golideyo kwa iwowo, ndizo zokometsera zonse zokonzeka.
52 Ndipo golide yense wa nsembe yokweza ya Yehova amene anapereka kwa Yehova, wofuma kwa atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo masekeli zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.
53 Popeza wankhondo yense anadzifunkhira yekha.
54 Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golide kwa akulu a zikwi ndi a mazana, nalowa naye kuchihema chokomanako, chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/31-1b000e536eb5cc4f18b92490cfc42ad3.mp3?version_id=1068—